Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

MARCH 5, 2020
NKHANI ZA PADZIKO LONSE

Khoti la ku Crimea Lagamula Kuti M’bale Sergey Filatov ndi Wolakwa Ndipo Akakhale M’ndende Zaka 6

Khoti la ku Crimea Lagamula Kuti M’bale Sergey Filatov ndi Wolakwa Ndipo Akakhale M’ndende Zaka 6

Pa 5 March, 2020, Khoti la m’boma la Dzhankoysky ku Republic of Crimea linagamula kuti M’bale Sergey Filatov ndi wolakwa. M’baleyu wagamulidwa kuti akakhale m’ndende zaka 6. M’bale Filatov ndi wa Mboni woyamba kupezeka wolakwa ku Crimea mogwirizana ndi Buku la Malamulo a Zaupandu la ku Russia. M’baleyu akapanga apilo chigamulochi.