Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

JUNE 4, 2020
NKHANI ZA PADZIKO LONSE

Khoti la ku Crimea Linagamula Kuti M’bale Artem Gerasimov Akhale M’ndende Zaka 6

Khoti la ku Crimea Linagamula Kuti M’bale Artem Gerasimov Akhale M’ndende Zaka 6

Pa 4 June 2020, Khoti Lalikulu Kwambiri ku Crimea linagamula kuti M’bale Artem Gerasimov akhale m’ndende zaka 6. M’baleyu anamangidwa chifukwa choti amalambira Mulungu ngakhale kuti ankachita zimenezi mwamtendere. Khoti la mumzinda wa Yalta ndi limene linazenga mlandu wakewu koyamba ndipo linagamula kuti alipire chindapusa cha ndalama zokwana madola pafupifupi 6,000 a ku America. Koma m’baleyu anakadandaula za nkhaniyi ku Khoti Lalikulu Kwambiri. Khotili litangopereka chigamulo chake, M’bale Gerasimov anakamutsekera m’ndende nthawi yomweyo. Komabe, iye akapanga apilo chigamulochi.