MARCH 31, 2020
NKHANI ZA PADZIKO LONSE
Kuthandiza Achikulire Kuti Apitirizebe Kuchita Zinthu Zokhudza Kulambira Panthawi ya Mliri
Anthu achikulire ali pangozi yaikulu yotenga matenda a kolonavairasi. Chifukwa cha zimenezi, abale ndi alongo athu achikulire akuchita zinthu mwanzeru pomvera malangizo a azachipatala, oti asamatuluke m’nyumba zawo. Komabe zimenezi sizikutanthauza kuti achikulirewa ali okha kapena kuti alibe zochita. Iwo akugwiritsa ntchito zipangizo zamakono kuti azichita nawo misonkhano komanso kulalikira.
Mwachitsanzo, mlongo wina wa mumzinda wa Rome ku Italy, wakaza 94 yemwe anabadwa mu 1952, wakhala asakuchoka panyumba ngakhale mliriwu usanayambe. Iye wakhala akuonera misonkhano pa JW Stream komabe anali asanaonerepo misonkhano ya mumpingo wake. Koma panopa akulu a mumpingo wake akumachititsa misonkhano yampingo yochita kulumikiza anthu pavidiyo. Zimenezi zathandiza kuti mlongoyu azichita nawo misonkhano yampingo wake komanso kuonana ndi abale ndi alongo.
Mlongo wina wa ku Spanish Fork ku Utah m’dziko la U.S.A, dzina lake Stephanie Aitken, ali ndi vuto lakumva ndipo amakhala kumalo osungirako anthu achikulire. Panopa sakulolanso kuti alendo azifika kumalowa. Mkulu wina limodzi ndi mkazi wake anathandiza mlongoyu kuika pa tabuleti yake pulogalamu yolumikizira pa vidiyo. Iwo ankapatsa mlongoyo malangizo oikira pulogalamuyo mu chinenero chamanja kudzera pa khomo la galasi la pamalowo. Mlongo Aitken atangomaliza kuika pulogalamuyo anahaga tabuleti yakeyo chifukwa cha chisangalalo. Iye akusangalala kwambiri kuti panopo akutha kulumikizana ndi abale ndi alongo mumpingo wake.
Panopo abale ndi alongo padziko lonse kuphatikizapo achikulire, akugwiritsa bwino ntchito zipangizo zamakono malinga ndi kusintha kwa zinthu chifukwa cha matenda omwe avutawa. Zimenezi zikutikumbutsa zimene Yehova analonjeza anthu ake kuti azidzagwiritsa ntchito mwanzeru “mkaka wa mitundu ya anthu.” (Yesaya 60:16) Tikudziwa kuti Yehova apitirizabe kupatsa atumiki ake a padziko lapansi chilichonse chimene angafune panthawi ya mavuto.
Banja lina ku Sweden (pamwamba chakumanzere), m’bale wa ku France (m’munsi chakumanzere) komanso banja lina ku South Korea (kumanja) ali pamisonkhano
Banja lina ku Norway likulalikira pafoni
Akulu akulimbikitsa banja ku Italy