Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

NOVEMBER 13, 2019
NKHANI ZA PADZIKO LONSE

Lipoti la Chaka cha Utumiki la 2019 Likusonyeza Kuti Anthu Ambiri Abatizidwa Kuposa Zaka 20 Zapitazo

Lipoti la Chaka cha Utumiki la 2019 Likusonyeza Kuti Anthu Ambiri Abatizidwa Kuposa Zaka 20 Zapitazo

Ndife osangalala kwambiri kulengeza kuti m’chaka cha utumiki cha 2019, anthu oposa 300,000 anabatizidwa n’kukhala a Mboni za Yehova. Aka ndi koyamba kuti chiwerengero cha anthu obatizidwa chipitirire 300,000 kuchokera m’chaka cha 1999. Tikuthokoza Yehova chifukwa chodalitsa ntchito yathu yolalikira ndi kupanga ophunzira yomwe timaigwira ndi mtima wathu wonse.

Pali zinthu zinanso zosaiwalika zomwe zinachitika m’chaka cha utumiki cha 2019 monga: misonkhano yamayiko, kutulutsidwa kwa Mabaibulo, komanso abale ndi alongo athu anasonyezana chikondi m’njira zosiyanasiyana. M’munsimu muli mbali ya ziwerengero zonse za mu lipoti la padziko lonse. *

  • Mayiko Amene Anatumiza Lipoti: 240

  • Opezeka pa Chikumbutso Padziko Lonse: 20,919,041

  • Ofalitsa Onse Amene Anagwira Ntchito Yolalikira: 8,683,117

  • Obatizidwa Onse: 303,866

Malipoti abwino ngati amenewa amatilimbikitsa kutsatira malangizo ochokera kwa Ambuye wathu Yesu omwenso akupezeka mu lemba lathu la chaka cha 2020 lakuti: “Pitani mukaphunzitse anthu . . . kuti akhale ophunzira anga. Muziwabatiza.”​—Mateyu 28:19.

^ Lipoti lonse la Chaka cha Utumiki cha 2019 la Mboni za Yehova liyamba kupezeka posachedwapa pa jw.org komanso pa pulogalamu ya JW Library.