JULY 3, 2020
NKHANI ZA PADZIKO LONSE
Mabaibulo 6 Anatulutsidwa pa 28 June 2020
A Mboni za Yehova akutulutsa Mabaibulo m’zilankhulo zatsopano pa nthawi ya mliri. Pa 28 June 2020, Baibulo la Dziko Latsopano linatulutsidwa m’zilankhulo izi: Chiswati, Chitsonga, Chizulu ndi Chitonga. Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki linamasuliridwanso mu Chikiriyo cha ku Belize ndi Chitotonaki. Ziletso zobwera chifukwa cha COVID-19 sizinalepheretse anthu kusangalala atalandira mabaibulowa pazipangizo zawo. Mabaibulowa anatulutsidwa pa nkhani zojambuliratu ndipo abale ndi alongo ankaonera pa stream kapena vidiyokomfelensi.
Chiswati, Chitsonga, ndi Chizulu
M’bale Geoffrey Jackson, wa m’Bungwe Lolamulira anatulutsa Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Opatulika m’Chiswati, Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Opatulika lokonzedwanso m’Chitsonga ndiponso m’Chizulu (onani chithunzi choyambirira). Ofalitsa ku South Africa ndi ku Eswatini analumikizidwa pa msonkhanowu.
M’gawo loyang’aniridwa ndi nthambi ya ku South Africa anthu pafupifupi 18.5 miliyoni amalankhula Chiswati, Chitsonga ndi Chizulu ndipo pa nambalayi pali ofalitsa oposa 38,000.
Chitonga (Malawi)
M’bale Augustine Semo, wa mu Komiti ya Nthambi ya ku Malawi analengeza za kutuluka kwa Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Opatulika la Chitonga (cha ku Malawi).
Abale ndi alongo omasulira anagwira ntchito zaka ziwiri kuti amasulire Baibulo la Chitonga. Womasulira wina ananena kuti: “Chitonga chilipo cha mitundu itatu. Zimene anthu amalankhula kwina sizimveka kwina. Ndiye tinkayesetsa kusankha mawu amene angamveke kwa anthu ambiri. Tinkaikanso mawu a m’munsi pofotokozera mawu amene si odziwika kwenikweni.”
Womasulira wina ananena kuti: “Ofalitsa sangavutike kugwiritsa ntchito Baibuloli muutumiki kapena pamisonkhano chifukwa ndi losavuta kumva komanso kuliwerenga.
Chikiriyo cha ku Belize
M’bale Joshua Killgore wa mu Komiti ya Nthambi ku Central America anatulutsa Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki mu Chikiriyo cha ku Belize. Panali anthu oposa 1,300 amene analumikizidwa ku pulogalamuyi.
Omasulira okwana 6 anagwira ntchito yomasulira Baibuloli kwa miyezi 16. Pofotokoza za Baibuloli, womasulira wina ananena kuti: “Tsopano abale ndi alongo athu ali ndi Baibulo lolondola komanso lodalirika. Lili ngati nyali yowathandiza kumvetsa Mawu a Mulungu.”
Womasulira wina ananena kuti: “Pa nthawi ya mliri wa COVID-19 abale ndi alongo amene amalankhula Chikiriyo cha ku Belize aziwerenga Malemba m’chilankhulo chawo. Izi ziwathandiza kuti mitima yawo ikhale m’malo komanso apirire mavuto amene akubwera.”
Ku Belize kuli ofalitsa 867 m’mipingo 19 ya Chikiriyo cha ku Belize. Palinso ofalitsa 58 amene ali m’gawo la chilankhulochi ku United States.
Chitotonaki
M’bale Jesse Pérez, wa mu Komiti ya Nthambi ku Central America anatulutsa Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki m’Chitotonaki. Anthu pafupifupi 2,200 a m’mipingo 50 ya chilankhulochi analumikizidwa kuti aonere pulogalamuyi.
Omasulira anamaliza ntchitoyi pa zaka zitatu ndi miyezi yochepa yokha. Baibulo limeneli lithandiza kwambiri polalikira Uthenga Wabwino kwa anthu oposa 250,000 amene amalankhula chilankhulochi ku Mexico.
Womasulira wina anati: Mosiyana ndi Mabaibulo ena achilankhulochi, Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki lili ndi mawu amene timagwiritsa ntchito polankhula. Tsopano sitingavutikenso pofotokozera anthu nkhani zosiyanasiyana za m’Baibulo.”
Womasulira wina ananena kuti: “Abale ndi alongo akhala akulakalaka Baibulo ngati limeneli. M’mbuyomu abale ndi alongo akhala akumasulira okha mawu a m’Baibulo kuchokera ku Chisipanishi kuti agwiritse ntchito pamisonkhano yamkati mwa mlungu. Tsopano sazimasuliranso Malemba Achigiriki.”
Chosangalatsa kwambiri ndi Baibuloli ndi chakuti lili ndi mawu a m’munsi ofotokozera mawu ena. Mawu a m’munsiwa amathandiza kuti anthu a m’madera ena azimvetsa mawu amene agwiritsidwa ntchito m’Baibuloli. Izi zimachititsa kuti anthu onse achilankhulochi azilikonda kwambiri
Tikusangalala kwambiri kuti abale ndi alongo athu alandira Mabaibulo m’chilankhulo chawo. Sitikukayikira kuti chikhulupiriro chawo chilimba pamene akugwiritsa ntchito lupanga la mzimu limeneli muutumiki komanso pophunzira paokha.—Aheberi 4:12.