26 JANUARY, 2022
NKHANI ZA PADZIKO LONSE
Mawu Ofotokozera Mavidiyo a Msonkhano Wachigawo Akuthandiza Kwambiri Anthu a Vuto Losaona Komanso Amene Amaona Movutikira
Chaka chino chikhala chachitatu kuti msonkhano wachigawo ukhale ndi mawu ofotokozera mavidiyo. Mavidiyo okhala ndi mawu ofotokozerawa, amafotokoza zimene zikuoneka pa zithunzi komanso zimene zikuchitika, ndipo amagwiritsidwa ntchito kwambiri ndi anthu amene ali ndi vuto losaona komanso amene amaona movutikira. A Mboni za Yehova akupitiriza kupanga mavidiyo okhala ndi mawu ofotokozera kuti uthenga wa m’Baibulo ufikire anthu pafupifupi 43 miliyoni omwe ali ndi vuto losaona komanso anthu 295 miliyoni omwe amaona movutikira.
Pulezidenti wa Audio Description Associates, LLC, Dr. Joel Snyder, omwe ndi katswiri wodziwika bwino pankhani yopanga mawu ofotokozera mavidiyo, anena kuti: “Ndine wosangalala kwambiri ndi zimene a Mboni za Yehova akuchita pothandiza kuti anthu amene ali ndi vuto losaona komanso amene amaona movutikira azipeza zinthu zimene zingawathandize mosavuta. Anthu ambiri akamapanga mavidiyo, saganizira zoika mawu ofotokozera kuti athandize anthu amene ali ndi vuto losaona. Choncho ndikufuna kuthokoza a Mboni za Yehova chifukwa chochita zimenezi.”
Bungwe Lolamulira litaganiza kuti msonkhano wachigawo wa 2020 ukhale wojambulidwa chifukwa cha mliriwu, linaganizanso kuti ukhale ndi mawu ofotokozera mavidiyo. Mu 2020 Dipatimenti Yothandiza Omasulira yomwe ili ku Likulu la Padziko Lonse la Mboni za Yehova ku Warwick, New York, U.S.A., inapanga mawu ofotokozera mavidiyo a msonkhanowu. Mu 2021, ntchitoyi inaperekedwa ku dipatimenti imene imakonza kaonekedwe ka mabuku yomwe ili ku Likulu la Maphunziro la Watchtower, ku Patterson, New York. Anthu amene amagwira ntchito yokonza mawu ofotokozera mavidiyo analandira maphunziro kudzera pa intaneti a mmene angagwirire bwino ntchito yawoyi.
Dr. Snyder ananena kuti, “mukhoza kuwaphunzitsa anthuwa kuti azifotokoza zinthu m’njira yothandiza kwambiri.” Ananena kuti zimene zimaphatikizapo “kugwiritsa ntchito mawu achidule, osavuta kumva komanso amene munthu yemwe akuwamvayo angawaganizire mosavuta.”
Timu imene imagwira ntchitoyi, choyamba imamvetsera vidiyo imene akufuna kuikira mawu ofotokozerayo. Samaonera vidiyoyo chifukwa amafuna amvetse mmene munthu amene ali ndi vuto losaona kapena amene amaona movutikira angamvere. Aliyense pa timupo amalemba zimene watolapo. Kenako amaoneranso vidiyoyo, ndipo amaona malo amene anthu mu vidiyomo sakulankhula, chifukwa amenewa ndi malo amene amaika mawu ofotokozera.
Kuika mawu ofotokozera pamene munthu sakulankhula muvidiyo, ndi ntchito yovuta kwambiri. Michael Millen amene amagwira nawo ntchito yoikira mawu ofotokozera mu mavidiyo ndi a Mboni za Yehova ananena kuti, “popeza malowa amakhala ochepa, timafunika kusankha zinthu zofunika kwambiri zimene zingathandize munthu kumvetsa mosavuta zimene zikuchitika muvidiyoyo. Timayesetsa kufotokozera nthawi, malo, anthu amene ali muvidiyomo komanso zimene zikuchitika.”
Iwo sayenera kufotokozera chilichonse chimene chikuoneka muvidiyomo. M’buku lawo lakuti The Visual Made Verbal, Dr. Snyder analangiza anthu ogwira ntchito yoika mawu ofotokozera kuti: “Musamafotokoze zinthu mokokomeza, koma mwachikatikati, ndipo muzilola kuti omvera anu aziganizira okha zonse zimene zikuchita muvidiyomo potengera zimene mwafotokozazo. Mwachitsanzo, simukuyenera kunena kuti: ‘Wakwiya,’ kapena ‘Wakhumudwa.’ Koma m’malomwake muzinena zangati: ‘Wakunga chibakera,’ kapena ‘Akulira.’”
Timu yoika mawu ofotokozera ikamaliza kulemba mawu amene akufunikira, munthu wina amaziwerenga n’kujambula. Amene akuwerengayo amayenera kuwerenga modekha ndipo asamasinthesinthe mawu. A Michael Millen ananena kuti: “Munthu amene akuwerengayo sakuyenera kulankhula ngati kuti akupikisana ndi anthu amene ali muvidiyomo. Ngati munthuyo akuwerenga mokokomeza kwambiri, zingapangitse anthu kuganiza kuti ndi mmodzi wa anthu amene ali muvidiyomo.”
Kenako amene amagwira ntchito yokonza mavidiyo amaikonza komaliza ndipo imatumizidwa ku ma ofesi onse a nthambi kuti nawonso akaimasulire m’zilankhulo zawo. A Millen ananena kuti pa misonkhano iwiri yachigawo yapitayi, ntchito yonse yokonza mawu ofotokozera vidiyo ya 1 miniti, inkawatengera maola atatu.
Pofika pano, a Mboni za Yehova amamasulira mabuku, mavidiyo komanso zinthu zongomvetsera zofotokoza Baibulo mu zilankhulo zoposa 1,000. Ngakhale kuti mawu ofotokozera mavidiyo sakuphatikizidwa pa chiwerengero cha zilankhulozi, ena amaona kuti ndi chilankhulo pachokha. A Millen ananena kuti, “Mawu ofotokozera mavidiyo ndi chilankhulo cha anthu a vuto losaona. Zithunzi za muvidiyo zimafotokozedwa kuti anthu a vuto losaona, athe kuziona m’maganizo.”
Timathokoza kwambiri Yehova chifukwa amaonetsetsa kuti anthu onse akulandira chakudya chauzimu chokwanira chimene chimawathandiza kukhala ndi chikhulupiriro cholimba.—Yesaya 65:13.