Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Abale ndi alongo omwe panopo ali m’ndende ku Russia ndi ku Crimea

3 JANUARY, 2022
NKHANI ZA PADZIKO LONSE

Mayiko Osiyanasiyana Atulutsa Chikalata Chopempha Maboma Ena Kuti Asiye Kuzunza a Mboni za Yehova

Mayiko Osiyanasiyana Atulutsa Chikalata Chopempha Maboma Ena Kuti Asiye Kuzunza a Mboni za Yehova

Pa 17 December 2021, mayiko omwe ali m’Bungwe la Mayiko Onse Loona za Zikhulupiriro Komanso Ufulu wa Zipembedzo, a (IRFBA) mogwirizana anatulutsa chikalata pofuna kuteteza a Mboni za Yehova omwe akuzunzidwa chifukwa chotsatira zomwe amakhulupirira. Chikalatachi chinapempha mayiko kuti amasule Amboni onse omwe ali m’ndende, komanso kuti asiye kuwazunza, kukafufuza zinthu m’nyumba zawo ndi kuwasala.

Padziko lonse, a Mboni za Yehova oposa 150 anatsekeredwa m’ndende chifukwa chotsatira zomwe amakhulupirira. Amboniwa anamangidwa m’mayiko monga Crimea, Eritrea, Russia, Singapore, ndi Tajikistan. Mayiko omwe ali m’Bungwe la Mayiko Onse Loona za Zikhulupiriro Komanso Ufulu wa Zipembedzo “anakhudzidwa kwambiri” ndi “kuchuluka kwa nkhanza” zomwe a Mboni za Yehova ena akukumana nazo. Bungweli linatinso a Mboni za Yehova ali ndi ufulu wotsatira zomwe amakhulupirira “popanda kuopsezedwa, kusalidwa kapenanso kuzunzidwa.”

Timayamikira maboma omwe amaganizira komanso kuteteza ufulu wathu wachipembedzo. Koposa zonse, tikudziwa kuti Yehova apitiriza kuteteza abale ndi alongo athu amene amamudalira ndipo adzapitiriza ‘kuwapatsa mtendere wosatha.’​—Yesaya 26:3.

a Bungweli linapangidwa ndi mayiko osiyanasiyana ndi cholinga chofuna kulimbikitsa zikhulupiriro ndi ufulu wa zipembedzo padziko lonse.