Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

FEBRUARY 19, 2020
NKHANI ZA PADZIKO LONSE

Mbali Yatsopano mu Pulogalamu ya JW Library Sign Language

Mbali Yatsopano mu Pulogalamu ya JW Library Sign Language

Mu pulogalamu ya JW Library Sign Language, Version 4, yomwe inatulutsidwa pa 15 February 2020, muli mbali yatsopano yofunika kwambiri. Mukamagwiritsa ntchito pulogalamu ya chinenero chamanja imeneyi, mukangodina kamodzi, malifalensi azioneka ndipo simuzivutika pokonzekera misonkhano yampingo komanso pofufuza mfundo zosiyanasiyana m’Baibulo.

Kwa nthawi yaitali pulogalamu ya JW Library ndi yomwe imatheka kufufuza zinthu pogwiritsa ntchito malinki osonyeza malemba a m’Baibulo kapena mabuku ndi zinthu zina popanda kutseka tsamba lomwe mwatsegulalo. Koma zimenezi zinali zosatheka mukamagwiritsa ntchito pulogalamu ya chinenero chamanja chifukwa panalibe njira yothandiza kuti izitsegula yokha nkhani ya vidiyo ndi malifalensi ake.

Koma panopa mu pulogalamu ya JW Library Sign Language, Version 4, malifalensi azioneka ngati malinki. Mukangodina kamodzi kokha, muzipeza malifalensi a mavidiyo owonjezera kenako muzitha kubwerera ku vidiyo yomwe munatsegula poyamba.

Onani njira yosavuta yothandiza kuona zinthu zokhudza misonkhano yamkati mwa mlungu

Tikukhulupirira kuti mbali yatsopanoyi ithandiza kwambiri abale ndi alongo athu omwe amadalira mabuku ndi zinthu zina za chinenero chamanja. Tili ndi zinthu zotithandiza kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova ndipo tikumuthokoza kwambiri chifukwa cha zimenezi.—Salimo 119:97.

Onani mmene lifalensi ya mawu akuti “njoka” pa Genesis 3:1 akusonyezera linki yopita pa Chivumbulutso 20:2 ndiponso mmene zikutithandizira kudziwa kuti “njoka yakale” ikuimira ndani