Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

OCTOBER 11, 2019
NKHANI ZA PADZIKO LONSE

Mfundo Zachidule Zokhudza Msonkhano Wapachaka wa 2019

Mfundo Zachidule Zokhudza Msonkhano Wapachaka wa 2019

Loweruka pa 5 October, 2019, bungwe la Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania linachita msonkhano wake wapachaka. Msonkhanowu unachitikira ku Nyumba ya Msonkhano ya Mboni za Yehova ku Newburgh, New York, U.S.A. Msonkhano wa bungweli utatha, Bungwe Lolamulira linafotokoza mfundo za m’Baibulo zolimbikitsa pamsonkhano womwe panapezeka anthu 20,679 kuphatikizapo ena omwe analumikizidwa m’malo ena. Mfundo zotsatirazi zikufotokoza mwachidule mbali iliyonse ya msonkhanowu. a

“Mtsogoleri Wanu Ndi Mmodzi, Khristu”

M’bale Gerrit Lösch yemwe anali tcheyamani wa pulogalamuyi anakamba nkhani yoyamba yochokera pa lemba la Mateyu 23:10, limene limatikumbutsa kuti Yesu Khristu ndiye mtsogoleri wathu osati munthu wina aliyense.

Yehova Amathandiza Pogwiritsa Ntchito Utumiki Wothandiza Anthu pa Nthawi ya Mavuto

M’bale Stephen Lett anafotokoza ubwino wopatsa ena zinthu mwachimwemwe. Njira imodzi imene tingasonyezere kuti tili ndi mtima wopatsa ndi kuchita nawo utumiki wothandiza anthu pa nthawi ya mavuto. M’bale Lett anafotokoza mwachidule zinthu zomwe zinaonongeka pa ngozi zamwadzidzidzi komanso chithandizo chimene chinaperekedwa m’chaka cha utumiki cha 2018 ndi cha 2019. Abale ndi alongo oposa 900,000 anakhudzidwa ndi ngozi zamwadzidzidzi zomwe zinachitika m’zaka zimenezi. Nyumba za Ufumu zopitirira 700 ndi nyumba za abale zopitirira 15,000 zinawonongeka kapena kugweratu. A Mboni za Yehova anagwiritsa ntchito ndalama zokwana madola 49.5 miliyoni a ku America pa utumiki wothandiza anthu pa nthawi ya mavutoyi.

Nkhaniyi inali ndi mavidiyo osonyeza ofalitsa omwe analandira chithandizo akuyamikira utumiki wothandiza anthu womwe umachitika pa nthawi ya mavuto.

‘Dzanja Labwino la Mulungu Wathu Lili pa Ife . . . Tiyeni Timange’ | Vidiyo

Vidiyoyi inafotokoza kuti a Mboni za Yehova amasamalira nyumba zosiyanasiyana pafupifupi 80,000 zomwe ali nazo padziko lonse. Inafotokozanso njira zomwe timagwiritsa ntchito posamalira, kukonza ndi kumanga nyumba zomwe gulu lathu limagwiritsa ntchito.

Zomwe Tachita pa Nkhani Yogula Malo Osiyanasiyana ndi Nyumba | Vidiyo

Mu vidiyoyi munalinso vidiyo yomwe inasungidwa yokhala ndi mbali yocheza ndi abale atatu omwe anathandiza nawo m’mbuyomu pa ntchito yosankha ndi kugula malo a nthambi ya United States komanso likulu lapadziko lonse. Abalewa ndi: M’bale Max Larson, M’bale George Couch, ndiponso M’bale Gilbert Nazaroff. Abale atatuwa anafotokoza umboni wosonyeza mmene Yehova anathandizira kuti tipeze malo osiyanasiyana ndi nyumba.

Pakukonzedwa Zomanga Beteli Yatsopano | Vidiyo

Mu vidiyoyi analengeza kuti a Mboni za Yehova akufuna kumanga Beteli yatsopano komwe kuzidzagwiridwa ntchito zojambula mavidiyo ndi zinthu zina. Beteliyi idzamangidwa ku Ramapo, New York. Malowa ali pamtunda wa makilomita atatu kuchokera ku likulu lathu ku Warwick, New York. Ntchito yomanga Beteli yatsopanoyi ikuyembekezeka kuyamba mu 2022 ndipo idzatha mu December 2026. Ntchitoyi ikadzafika pachimake pazidzafunika antchito odzipereka pafupifupi 1,500 tsiku lililonse.

Chithunzi chosonyeza mmene Beteli yatsopano yomwe idzamangidwe ku Ramapo, New York, idzaonekere. Pamalowa padzakhala situdiyo, maofesi, nyumba zogona, ndiponso malo ofotokoza zinthu zomwe alendo angaone

Pulogalamu Yatsopano Yothandiza Pofunsira Mautumiki | Vidiyo

Vidiyoyi inafotokoza kuti kuyambira mu January 2020, ofalitsa omwe akufuna kuonjezera utumiki wawo azitha kusaina mafomu kudzera pa jw.org ndi kuwatumiza ku bungwe la akulu la mpingo wawo.

Njira Yatsopano Yopezera Zinthu Zongojambulidwa pa JW.ORG

Tsopano muzitha kupeza zinthu zongomvetsera zomwe mwasankha pa jw.org pogwiritsa ntchito Amazon Alexa kapena Google Assistant.

Gulu Lankhondo Lochokera Kumpoto

M’bale David Splane anafotokoza kamvedwe katsopano ka ulosi wopezeka mu chaputala 2 cha Yoweli, wofotokoza za dzombe. Tikuyembekezera mwachidwi kudzaphunzira mfundo zatsopano zokhudza ulosi umenewu ukadzafotokozedwa mu Nsanja ya Olonda.

Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika (Lothandiza Pophunzira) kuyambira Mateyu mpaka Machitidwe

Gwiritsirani Ntchito Baibulo Lophunzirira Pophunzira Baibulo

M’bale Samuel Herd anafotokoza ubwino wa Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika (Lothandiza Pophunzira) lomwe likupezeka pa webusaiti yathu. Kenako anatulutsa Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika (Lothandiza Pophunzira) losindikizidwa lokhala ndi mabuku a Mateyu mpaka Machitidwe. Ofalitsa angaitanitse Baibuloli kudzera kumpingo wawo.

Tili ndi Ntchito Yoti Tigwire!

M’bale Anthony Morris anatsindika mfundo yoti ntchito yofunika kwambiri ya Akhristu oona ndi yolalikira uthenga wabwino. Maofesi a nthambi ndi malo ena omwe gulu lathu linamanga amathandiza Bungwe Lolamulira poyendetsa ntchito yolalikira komanso kupereka chakudya chauzimu kwa anthu a Yehova. M’bale Morris anagwira mawu osangalatsa kwambiri a mu Nsanja ya Olonda ya November 15, 1976, akuti: “Pa nthawi imene ‘chisautso chachikulu’ chizidzafika, tikufunika kudzakhala otanganidwa kwambiri ndi ntchito yolalikira kusiyana ndi kale lonse. Ambuye Yesu akadzafika kudzapereka chiweruzo, aliyense adzadzidzimuka kwambiri. Nawonso anthu a Yehova adzadzidzimuka chifukwa pa nthawiyi adzakhala otanganidwa kwambiri kuchita chifuniro cha Yehova.”

Kodi Tiziopa Ndani?

M’bale Mark Sanderson anafotokoza kuti Yesu analosera kuti anthu a Mulungu amayembekezera kudedwa ndi “mitundu yonse.” (Mateyu 24:9) Komabe, M’bale Sanderson anatilimbikitsa kuti tisamaope anthu koma tiziopa Yehova.—Salimo 111:10.

Panawonetsedwa vidiyo yokhudza mtima yosonyeza abale ndi alongo omwe anazunzidwa ku Russia akufotokoza zimene zinawathandiza kuti asamaope kuzunzidwa. Nkhaniyi komanso vidiyoyi zinalimbikitsa kwambiri anthu a Yehova kuti nawonso asamaope kuzunzidwa.

Kodi Ndinu Woganiza Bwino?

M’bale Geoffrey Jackson anafotokoza mmene tingagwiritsire ntchito mavesi opezeka m’Malemba Achigiriki omwe ali ndi mawu otanthauza “kuganiza bwino.” M’baleyu anatsindikanso kufunika kopitiriza ‘kukhalabe oganiza bwino’ m’masiku otsiriza ano.—1 Petulo 1:13.

Kodi Mudzagwira Nawo Ntchitoyi?

M’bale Kenneth Cook analengeza lemba la chaka cha 2020, lomwe ndi la Mateyu 28:19. Lembali limati: Pitani mukaphunzitse anthu . . .  kuti akhale ophunzira anga. Muziwabatiza.” M’baleyu anatsindika kufunika kothandiza anthu a mtima wabwino kuti adzipereke kwa Yehova ndi kubatizidwa.

Misonkhano ngati imeneyi imatilimbikitsa kuti tipitirize kutumikira Yehova modzipereka.

a Pulogalamu yonse ya msonkhano wapachaka idzaikidwa pa jw.org mu January 2020.