26 SEPTEMBER, 2022
NKHANI ZA PADZIKO LONSE
Mkuntho wa Fiona Unawononga ku Caribbean
Pa 18 September 2022, mphepo yamkuntho ya Fiona inadutsa ku Puerto Rico komanso kuzilumba zoyandikana ndi dzikoli. Mphepoyi inkathamanga pamtunda wa makilomita 160 pa ola limodzi ndipo madzi a mvula analowa pansi kufika masentimita 75. Mkunthowu unawononga misewu, mabuliji komanso zipangizo zamagetsi. Akuluakulu aboma akukumana ndi mavuto aakulu akamakapereka chakudya, madzi komanso mankhwala kwa anthu okhudzidwa chifukwa cha kuwonongeka kwa misewu ndi mabuliji.
Mmene zakhudzira abale ndi alongo athu
Puerto Rico, Saint Kitts and Nevis komanso Turks and Caicos
Palibe m’bale kapena mlongo aliyense amene anafa pangoziyi
Ofalitsa 4 anavulala pang’ono
Ofalitsa 75 anasamuka m’nyumba zawo
Nyumba 140 zinawonongeka pang’ono
Nyumba 18 zinawonongeka kwambiri
Nyumba imodzi inawonongekeratu
Ku Dominican Republic
Palibe m’bale kapena mlongo aliyense amene anafa pangoziyi
Ofalitsa 58 anasamuka m’nyumba zawo
Nyumba 57 zinawonongeka pang’ono
Nyumba 26 zinawonongeka kwambiri
Nyumba ziwiri zinawonongekeratu
Nyumba za Ufumu ziwiri zinaonongeka pang’ono
Nyumba za Ufumu ziwiri zinaonongeka kwambiri
Ku Guadeloupe ndi ku Martinique
Palibe m’bale kapena mlongo aliyense amene anafa pangoziyi
Ofalitsa 16 anasamuka m’nyumba zawo
Nyumba 43 zinawonongeka pang’ono
Nyumba ziwiri zinawonongeka kwambiri
Nyumba za Ufumu 13 zinaonongeka pang’ono
Ntchito Yopereka Chithandizo
Oyang’anira madera komanso akulu akumadera okhudzidwawa, akuchititsa maulendo aubusa kwa mabanja amene anakhudzidwa ndi ngoziyi komanso kuwapatsa chithandizo
Ntchito yopereka chakudya, madzi, mankhwala komanso yokonza nyumba za abale zimene zinawonongeka ili mkati.
Ntchito yopereka chithandizoyi ikugwiridwa motsatira njira zonse zodzitetezera ku COVID-19
Tikudziwa kuti abale ndi alongo amene anakhudzidwa ndi ngoziyi atonthozedwa chifukwa cha chikondi chachikulu chimene abale ndi alongo amasonyezana.—Machitidwe 11:29.