2 OCTOBER 2024
NKHANI ZA PADZIKO LONSE
Mphepo Yamkuntho ya Boris Yachititsa Kuti Madzi Asefukire Kwambiri M’madera Ena a ku Central Europe
Kuyambira pa 11 September 2024, Mphepo yamkuntho ya Boris inachititsa kuti m’mayiko ena a ku Central Europe kugwe mvula yambiri komanso kuwombe mphepo yamphamvu kwambiri. Pamene mphepoyi inkawomba kum’mwera kwa dziko la Poland pa 12 September, madera ena analandira mvula yambiri yokwana masentimita 20 m’nthawi yosakwana maola 24, ndipo madzi anasefukira m’madera ambiri. Mvula yamphamvu yomwe inagwa kwa nthawi yaitaliyi, inawononganso zinthu zambiri moti anthu masauzande ambiri anakhala opanda magetsi. Tsiku lotsatira pa 13 September, mphepo ya Boris inachititsa kuti madera akumpoto kwa dziko la Czech Republic alandire mvula yochuluka kwambiri yokwana masentimita oposa 50, ndipo nyumba, misewu komanso mabuliji zinawonongeka kwambiri.
Kenako pa 14 September, m’midzi yambiri ya ku Romania kunasefukira madzi pamene kunagwa mvula yochuluka kukwana masentimita 25. Nyumba 5,000 zinawonongeka komanso madamu awiri anaphulika chifukwa cha kuchuluka kwa madzi ku Galați County. Pa 18 September, mphepo ya Boris inafika kumpoto kwa dziko la Italy. M’madera ambiri munagwa mvula yokwana pafupifupi masentimita 30 m’maola 48 okha ndipo mitsinje yambiri inasefukira.
Mphepo yamphamvu kwambiriyi inachititsa kuti anthu masauzande ambiri achoke m’nyumba zawo m’mayiko onse 4 amenewa ndipo anthu 19 anafa.
Mmene Mphepoyi Yakhudzira Abale Ndi Alongo Athu
Ku Czech Republic
Palibe m’bale kapena mlongo wathu aliyense amene anavulala kapena kufa
Ofalitsa 79 anasowa pokhala
Nyumba 12 zinawonongeka kwambiri
Nyumba ziwiri zinawonongeka pang’ono
Nyumba ya Ufumu imodzi inawonongeka kwambiri
Nyumba ya Ufumu imodzi inawonongeka pang’ono
Ku Italy
Palibe m’bale kapena mlongo wathu aliyense amene anavulala kapena kufa
Ofalitsa 63 anasowa pokhala
Nyumba 7 zinawonongeka kwambiri
Nyumba 21 zinawonongeka pang’ono
Nyumba ya Ufumu imodzi inawonongeka kwambiri
Nyumba za Ufumu 4 zinawonongeka pang’ono
Ku Poland
Palibe m’bale kapena mlongo wathu aliyense amene anavulala kapena kufa
Ofalitsa 87 anasowa pokhala
Nyumba 61 zinawonongeka kwambiri
Nyumba 85 zinawonongeka pang’ono
Nyumba za Ufumu ziwiri zinawonongeka kwambiri
Nyumba za Ufumu 8 zinawonongeka pang’ono
Ku Romania
Palibe m’bale kapena mlongo wathu aliyense amene anavulala kapena kufa
Ofalitsa mmodzi anasowa pokhala
Nyumba ziwiri zinawonongeka kwambiri
Nyumba 5 zinawonongeka pang’ono
Palibe Nyumba ya Ufumu imene inawonongeka kapena kugwa
Ntchito Yothandiza Anthu
Panakonzedwa Makomiti Othandiza Pakachitika Ngozi Zamwadzidzidzi okwana 6 kuti atsogolere pa ntchito yothandiza anthu
Oyang’anira madera komanso akulu akulimbikitsa anthu amene akhudzidwa pogwiritsa ntchito Baibulo komanso kuwathandiza m’njira zina
Pamene tikupitiriza kupempherera anthu amene akhudzidwawa, tikukhulupirira kuti, mwachikondi, Yehova awathandiza komanso kuwalimbikitsa.—Yesaya 40:11.