4 OCTOBER, 2022
NKHANI ZA PADZIKO LONSE
Mphepo Yamkuntho ya Ian Yawononga Kwambiri
Pa 27 September 2022, mphepo yamkuntho ya Ian inawononga kwambiri ku Cuba. Mawa lake inakawombanso mwamphamvu kwambiri m’chigawo chakum’mwera chakumadzulo kwa Florida. Mkunthowu womwe unkawomba pa liwiro la makilomita 240 pa ola limodzi, unali umodzi wa mikuntho yamphamvu koopsa pa mikuntho yomwe inawombapo ku Unites States. Mphepoyi inawononga dera lonse ndipo dera lalikulu kunalibe magetsi, misewu komanso mabuliji zinawonongeka ndipo madzi anasefukira kukafika ku Atlantic Ocean. Pambuyo pake mkunthowu unakawombanso ku South Carolina.
Mphepo yoopsayi yachititsa kuti ofalitsa a ku Florida oposa 12,000 asowe pokhala kapena asamuke m’nyumba zawo.
Oyang’anira madera akugwira ntchito limodzi ndi a Dipatimenti Yoona za Mapulani ndi Zomangamanga pothandiza akulu kusamalira abale ndi alongo amene akhudzidwa ndi mphepoyi.
Mmene Zakhudzira Abale ndi Alongo Athu
Ku Cuba
N’zomvetsa chisoni kuti m’bale mmodzi anafa
Abale awiri anavulala pang’ono
Nyumba 300 zinawonongeka pang’ono
Nyumba 491 zinawonongeka kwambiri
Nyumba 63 zinawonongekeratu
Malo ochitira misonkhano okwana 40 anawonongeka pang’ono
Malo amodzi ochitirapo msonkhano anawonongeka pang’ono
Malo atatu ochitirapo msonkhano anawonongeka kwambiri
Ku Florida
Abale ndi alongo athu sanavulale
Ofalitsa awiri anavulala pang’ono
Panopa, ofalitsa 5,874 akusowa pokhala
Nyumba 1,559 zinawonongeka pang’ono
Nyumba 367 zinawonongeka kwambiri
Nyumba 47 zinawonongekeratu
Nyumba 329 zinakonzedwa ndipo anthu anayambanso kukhalamo
Nyumba 71 zinakonzedwa
Nyumba 38 zomwe zinkagwiritsidwa ntchito ndi Mboni za Yehova zinawonongeka pang’ono
Nyumba ya Ufumu imodzi inawonongeka kwambiri
Malo amodzi ochitirapo msonkhano anawonongeka kwambiri
Ku South Carolina
Palibe m’bale kapena mlongo aliyense amene anavulala kapena kufa ndi mphepo yamkunthoyi
Ofalitsa 35 anathawa m’nyumba zawo
Nyumba 13 zinawonongeka pang’ono
Ntchito Yopereka Chithandizo
Oyang’anira madera komanso akulu akulimbikitsa mabanja amene anakhudzidwa komanso kuwapatsa zinthu zofunikira
Kunakhazikitsidwa malo 14 othandizirapo abale ndi alongo omwe anathawa m’nyumba zawo
Ku Florida ndi ku Cuba kunakhazikitsidwa Makomiti Othandiza Pangozi Zamwadzidzidzi kuti aziyang’anira ntchito yothandiza anthu
Ntchito zonse zopereka chithandizo, zikugwiridwa potsatira njira zopewera COVID-19
Pomwe abale athu akuthandiza Akhristu anzawo panthawi yamavuto, tikuona kukwaniritsidwa kwa mawu a wamasalimo akuti: “Wokhulupirira Yehova amazunguliridwa ndi kukoma mtima kosatha.”—Salimo 32:10.