APRIL 19, 2021
NKHANI ZA PADZIKO LONSE
Mphepo Yamkuntho ya Seroja Yawononga ku Indonesia ndi ku Timor-Leste
Malo
Kuzilumba za East Nusa Tenggara kum’mawa kwa Indonesia ndi Timor-Leste
Ngozi yake
Pa 4 April 2021, mphepo yamkuntho yotchedwa Seroja inawononga m’madera ambiri komanso anthu anafunika kusamuka m’nyumba zawo
Mmene ngoziyi yakhudzira abale ndi alongo athu
Anthu osachepera 236 anachoka m’nyumba zawo
Katundu amene wawonongeka
Indonesia
Nyumba 45 zinawonongeka pang’ono
Nyumba 8 zinawonongeka kwambiri
Nyumba za Ufumu zitatu zinawonongeka pang’ono
Timor-Leste
Nyumba 19 zinawonongeka pang’ono
Nyumba 10 zinawonongeka kwambiri
Ntchito yothandiza anthu
Ku Indonesia, Komiti Yothandiza Pakachitika Ngozi Zadzidzidzi inakhazikitsidwa kuti iyendetse ntchito yothandiza anthu. Komitiyi ikuyendetsa ntchito yokonza Nyumba za Ufumu zimene zinawonongeka komanso nyumba za anthu zimene zinawonongeka kwambiri
Oyang’anira madera akugwiritsa ntchito Mawu a Mulungu polimbikitsa abale ndi alongo amene anakhudzidwa ndi ngoziyi
Ngoziyi itangochitika, mwamsanga akulu amumpingo anapezera malo okhala abale ndi alongo omwe anakhudzidwa. Komanso, akuluwa anagawira abale ndi alongo chakudya, madzi ndi zinthu zina zofunikira. Kuwonjezera pamenepo, iwo anathandizanso pa ntchito yokonza nyumba zimene zinawonongeka
Ku Timor-Leste, akulu ayamba kale kuyendetsa ntchito yokonza nyumba zimene zinawonongeka komanso kugawa chakudya ndiponso zinthu zina zofunika kwa anthu amene anakhudzidwa ndi ngoziyi. Akuluwa apezeranso anthu amene anakhudzidwa ndi ngoziyi malo ongoyembekezera oti akhalemo
Pogwira ntchitoyi, abale ndi alongo onse akuyesetsa kuchita zinthu mosamala potsatira malangizo opewera mliri wa COVID-19
Tikuthokoza kwambiri Yehova chifukwa choti akutithandiza kudzera mu utumiki wothandiza anthu umene abale ndi alongo m’mipingo akuchita.—2 Akorinto 9:13.