SEPTEMBER 3, 2020
NKHANI ZA PADZIKO LONSE
Msonkhano Woyamba Wochita Kujambulidwa Unachitika Padziko Lonse mu 2020
M’mwezi wonse wa July ndi August 2020, abale ndi alongo mamiliyoni ambiri komanso anthu ena omwe amafuna kuphunzira za Yehova anaonera msonkhano wa 2020 wochita kujambulidwa.
Kwa nthawi yaitali, a Mboni za Yehova ankayembekezera mwachidwi kuti adzachite msonkhano wamutu wakuti “Kondwerani Nthawi Zonse.” Monga mwa nthawi zonse, msonkhanowu unkayenera kuchitikira m’Malo a Misonkhano, m’masitediyamu komanso malo ena m’mayiko okwana 240. Koma pofuna kuteteza anthu kuti asatenge matenda, Bungwe Lolamulira linasankha kuti msonkhanowu ungokhala wochita kujambulidwa ndipo anthu padziko lonse adzangoonera pa zipangizo zawo. Aka n’koyamba kuti msonkhano uchitike mwanjira imeneyi kuyambira mu 1897.
M’bale Kenneth Cook, Jr. wa m’Bungwe Lolamulira anati: “Zitangodziwika kuti msonkhanowu ukhala wochita kujambulidwa, cholinga chathu chinali choti tonse tidzaonere pa nthawi yofanana. Tinkadziwa kuti msonkhanowu ukuyenera kumasuliridwa m’zinenero mahandiredi ambiri pa miyezi yosakwana 4. Koma kunena zoona, ntchito imeneyi si yamasewera ayi moti ikanatha kutenga chaka kapena kuposa pamenepo kuti ithe. Ngakhale panali ntchito yaikulu chonchi, tinasangalala kwambiri pamene mbali yoyamba ya msonkhanowu inatulutsidwa m’zinenero pafupifupi 400 pa 6 July 2020. Tikuyembekezera kuti msonkhanowu umasuliridwa m’zinenero 511.”
Pofotokoza ubwino wa msonkhano wongojambulidwawu, mlongo wina yemwe amalera yekha ana atatu anati: “N’zoona kuti tawasowa kwambiri anzathu omwe timasonkhana nawo, komabe njira imeneyi yathandiza ana anga. Kuonera msonkhanowu m’zigawo zing’onozing’ono kwawathandiza kuti azimvetsera mwatcheru. Akatopa, timangoimitsa kaye n’kupuma ndipo saphonya mfundo iliyonse. Chigawo cha Lachisanu chinanena kuti ana ali ngati mivi ndipo tiyenera kuwathandiza kuti akamakula azikhala ndi cholinga chodzatumikira Yehova mosangalala. Msonkhano wojambulidwawu ukundithandiza kuchita zimenezi.”—Salimo 127:4.
Atolankhani am’mayiko osiyanasiyana anachita chidwi kwambiri ndi msonkhano umenewu. Mwachitsanzo, M’bale Robert Hendriks, yemwe amayang’anira Dipatimenti Yoona Zofalitsa Nkhani ku United States, anati: “Atolankhani ambiri analemba nkhani zokhudza msonkhano wongochita kujambulawu. Iwo anayamikira kwambiri gulu lathu pogwiritsa ntchito njira zamakono n’cholinga choti anthu aonere msonkhanowu ali otetezeka.”
Msonkhano wa 2020 wamutu wakuti “Kondwerani Nthawi Zonse,” watithandiza kuona m’njira yatsopano komanso yosangalatsa kwambiri kuti Yehova Mulungu wathu ndi Mlangizi Wamkulu.—Yesaya 30:20.