Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

APRIL 29, 2020
NKHANI ZA PADZIKO LONSE

Mwambo Wokumbukira Imfa ya Khristu wa 2020—Zithunzi Zochokera M’mayiko Osiyanasiyana

Ngakhale Kuti Sanakumane Pamodzi, Abale ndi Alongo Padziko Lonse Anachita Zinthu Mogwirizana

Mwambo Wokumbukira Imfa ya Khristu wa 2020—Zithunzi Zochokera M’mayiko Osiyanasiyana

Pamene dzuwa linkalowa pa 7 April 2020, abale ndi alongo athu padziko lonse anachita mwambo wosaiwalika wa Chikumbutso. Ngakhale kuti mliri unachititsa kuti anthu ambiri asakumane pamodzi pa nthawiyi, aliyense anamvera lamulo la Yesu lakuti “muzichita zimenezi pondikumbukira.” (Luka 22:19) Abale ndi alongo athu onse, kaya amakhala okha, mabanja, makolo omwe ali ndi ana kuphatikizaponso achikulire athu omwe timawakonda, anachita zinthu mogwirizana posonyeza kuyamikira Yehova ndi Mwana wake, Yesu Khristu.

Zithunzi zotsatirazi zikusonyeza abale ndi alongo athu padziko lonse akukonzekera komanso akuchita Mwambo Wokumbukira Imfa ya Khristu wa 2020.