APRIL 16, 2020
NKHANI ZA PADZIKO LONSE
Mwambo Wokumbukira Imfa ya Khristu wa 2020—ku Africa
Unaulutsidwa pa TV ndi pa Wailesi
Chaka chino, Mwambo Wokumbukira Imfa ya Khristu unali wapadera. Kanali koyamba kuti mwambo wa Chikumbutso uwulutsidwe pa ma TV ndi pa mawailesi m’zinenero zosiyanasiyana komanso m’madera ambirimbiri a ku Africa.
Ofalitsa oposa 407,000 anaonera mwambo wa Chikumbutsowu ndipo anthu enanso achidwi anaonera kapena kumvetsera nawo. Ngakhale kuti chiwerengero chonse cha anthu omwe anaonera sizichikudziwika, anthu omwe amakhala m’maderawa ndi oposa 150 miliyoni.
Chifukwa cha mliri wa COVID-19, anthu ambiri padziko lonse anaonera mwambo wa Chikumbutso kudzera pa vidiyokomfelensi. Koma ofalitsa ambiri ku Africa amakhala m’madera omwe mitengo ya intaneti ndiponso telefoni ndi yokwera ndipo zimakhala zovuta kuti aonere kapena kupanga dawunilodi mavidiyo pa intaneti. Poganizira zimenezi, Bungwe Lolamulira linavomereza kuti maofesi ena a nthambi akambirane ndi nyumba zoulutsa mawu pa TV komanso pa wailesi kuti adzaulutse mwambowu pamitengo yabwino.
Tsiku la mwambowu lisanafike, abale m’maofesi a nthambi 11 ku Angola, Benin, Cameroon, Côte d’Ivoire, Democratic Republic of the Congo, Ghana, Malawi, Mozambique, Senegal, Zambia, ndi Zimbabwe, analumikizana ndi makampani oulutsa mawu n’kukonza zoti nkhani ya Chikumbutso idzaulutsidwe m’madera oposa 36 m’mayiko 16.
Ku Angola
Mawailesi 6 anavomera kuti aulutsa mwambo wa Chikumbutso m’zinenero 6. Zinenerozi ndi: Ibinda, Kikongo, Kimbundu, Nyaneka, Portuguese, ndi Umbundu. Mauthenga omwe mawailesiwa amafalitsa, amafika m’madera omwe mumakhala anthu ochuluka m’dzikolo.
Ku Democratic Republic of the Congo
Wophunzira Baibulo wina anakonza zoti aonere payekha mwambo wa Chikumbutsochi chifukwa choti anthu a m’banja lake amadana ndi a Mboni za Yehova. Komabe, pamene ankakonzekera kuti aonere nkhani ya Chikumbutso, bambo ake anamuitana n’kumuuza kuti: “Yayamba!” Atapita, anadabwa kuona kuti banja lonse lakhala pansi kuti lionere mwambo wa Chikumbutso pa TV. Anthu 10 a m’banjali anaonera Chikumbutsochi.
Munthu wina yemwe amakhala m’mudzi wa kufupi ndi ku Luena, anati: “Azibusa athu sanachite chilichonse. Koma inu mukupitirizabe kulambira Mulungu wanu ngakhale pa nthawi ya mliri wa COVID-19. Tikhala nanu limodzi!”
Ku Ghana
Wailesi yakanema ya m’dzikoli inavomera kuonetsa mwambo wa Chikumbutsowu m’chinenero cha Chitwi. Ndipotu pakanemayu ankaonetsaponso uthenga woitanira anthu kuti asadzalephere kuonera nawo mwambowu. Pambuyo poonetsa mwambowo, wailesi yakanemayi inaonetsanso mavidiyo akuti, N’chifukwa Chiyani Yesu Anafa? Komanso yakuti, N’chifukwa Chiyani Mulungu Amalola Kuti Anthu Azivutika?, kuphatikizaponso mavidiyo a nyimbo akuti, Dziko Latsopano Limene Likubwera ndi yakuti, Dziko Latsopano Lili Pafupi.
Ku Senegal
Mlongo wina anati: “Anthu anaphunzira za Yehova pa TV ndi pawailesi. Zimenezi n’zochititsa chidwi kwambiri! Tasangalala kwabasi ndipo tikunyadira kuti Mulungu wathu ndi Yehova!”
Mlongo winanso anati: “Titangomva zoti nkhani ya Chikumbutso idzaulutsidwa pa TV, mumtimamu ndinati: ‘Umenewu ndi mwayi wathu popeza sitinathe kuitanira anthu ku Chikumbutso chifukwa cha COVID-19.’ Nthawi yomweyo ndinadziwitsa ophunzira Baibulo anga, maulendo anga obwereza, komanso anzanga ena omwe si Mboni. Ophunzira Baibulo anga 9 anaonera nkhaniyi limodzi ndi mabanja awo. Msuweni wanga wina m’tawuni Ziguinchor ataonera nkhaniyi pa TV anandipempha kuti akufuna kudziwa zambiri pa nkhaniyo ndipo ndinavomera.”
Dongosolo lapaderali likusonyeza umboni winanso woti “zinthu zonse n’zotheka” kwa Yehova.—Mateyu 19:26.