Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

APRIL 16, 2021
NKHANI ZA PADZIKO LONSE

Mwambo Wokumbukira Imfa ya Yesu wa 2021​—Zithunzi Zochokera Padziko Lonse

Mwambo Wokumbukira Imfa ya Yesu wa 2021​—Zithunzi Zochokera Padziko Lonse

Pa 27 March 2021, a Mboni za Yehova padziko lonse anachita mwambo wokumbukira imfa ya Khristu pofuna kuthokoza zimene Yehova ndi Mwana wake Yesu Khristu anawachitira. Kwa zaka ziwiri tsopano mliri unalepheretsa abale ndi alongo kukumana pamasom’pamaso kuti achite mwambowu. Komabe, onse anali otsimikiza kumvera lamulo la Yesu lakuti: “Muzichita zimenezi pondikumbukira.”​—Luka 22:19.

Onani zithunzi m’munsimu zosonyeza abale ndi alongo athu padziko lonse akukonzekera komanso kuchita mwambo wa Chikumbutso cha 2021.