9 FEBRUARY, 2022
NKHANI ZA PADZIKO LONSE
Namondwe wa Ana Anawononga Kum’mwera Chakum’mawa kwa Africa
Kuyambira pa 24 mpaka pa 25 January 2022, madzi osefukira komanso mphepo yamphamvu zomwe zinachitika chifukwa cha namondwe wotchedwa Ana, zinawononga kwambiri m’dziko la Malawi ndi Mozambique. Namondweyu anapha anthu ambiri, kugumula misewu ndipo anthu masauzande anasowa malo okhala.
Mmene Zinakhudzira Abale ndi Alongo Athu
Malawi
N’zomvetsa chisoni kuti mkazi (sanali Wamboni) wa m’bale wathu wina komanso anawo awo awiri, wina wazaka zitatu ndi wina wazaka 5, anafa boti lopulumutsa anthu pangozi lomwe anakwera litagubuduka
Mlongo mmodzi ndi mwana wina wamkazi wazaka 7 amene makolo ake ndi Amboni, anavulala
Ofalitsa okwana 1,000 anakakamizika kusamuka m’nyumba zawo
Nyumba za Ufumu ziwiri zinawonongeka pang’ono
Nyumba za abale zokwana 100 zinawonongeka kwambiri
Nyumba za abale pafupifupi 100 zinawonongekeratu
Mozambique
Palibe m’bale kapena mlongo aliyense amene anafa pangoziyi
Abale awiri anavulala
Ofalitsa pafupifupi 381 anakakamizika kusamuka m’nyumba zawo
Nyumba za Ufumu zitatu zinawonongeka pang’ono
Nyumba za Ufumu zitatu zinawonongeka kwambiri
Nyumba za Ufumu zitatu zinawonongekeratu
Nyumba 51 za abale zinawonongeka pang’ono
Nyumba 96 za abale zinawonongeka kwambiri
Nyumba 79 za abale zinawonongekeratu
Ntchito Yopereka Chithandizo
Makomiti Othandiza pa Ngozi Zamwadzidzidzi, anakhazikitsidwa m’mayikowa
Makomitiwa anapereka chakudya, madzi akumwa aukhondo komanso thandizo lina lofunika
Onse ogwira ntchito yopereka chithandizoyi, ankatsatira njira zodzitetezera ku COVID-19
Tili ndi chikhulupiriro kuti Yehova athandiza abale athu onse omwe anakhudzidwa pa nthawi yovutayi.—Salimo 46:1.