Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

AUGUST 31, 2020
NKHANI ZA PADZIKO LONSE

Nkhani Zikuluzikulu Zomwe Zachitika M’chaka cha Utumiki cha 2020

Nkhani Zikuluzikulu Zomwe Zachitika M’chaka cha Utumiki cha 2020

M’chaka cha utumiki cha 2020, a Mboni za Yehova padziko lonse lapansi anakumana ndi mavuto achilendo potumikira Mulungu. Koma mavuto amenewa anasonyeza kuti abale ndi alongo athu ndi ofunitsitsa kukhalabe okhulupirika ndiponso ogwirizana.

Mavuto ambiri anayamba chifukwa cha mliri wa COVID-19, umene wasokoneza kwambiri zinthu padziko lonse m’njira imene sinachitikepo kwa nthawi yaitali.

Mliriwu utangoyamba, a Mboni za Yehova anasintha zinthu nthawi yomweyo. Iwo anapeza njira zatsopano zochitira misonkhano, kulimbikitsana ndiponso kulalikira uthenga wabwino.

Tiyeni tione “uthenga wabwino” wa zinthu zimene zinachitika m’chaka chosaiwalikachi.​—Miyambo 15:30.

Kutulutsa Mabaibulo

M’chaka cha utumiki chimenechi, gulu lathu linatulutsa Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Opatulika lathunthu kapena mbali yake m’zinenero 36. Chifukwa cha ziletso zobwera ndi mliri wa COVID-19, Mabaibulo ambiri anatulutsidwa pa zipangizo zamakono, pa misonkhano yochita kujambula. Panopa Baibulo la Dziko Latsopano likupezeka lathunthu kapena mbali yake m’zinenero 193.

Malipoti Ochokera ku Bungwe Lolamulira

Kuyambira pa 18 March 2020, abale a m’Bungwe Lolamulira akhala akupereka malipoti apadera okhudza mliriwu mwezi uliwonse pa jw.org ndi JW Library.

Mulipoti loyamba, M’bale Stephen Lett ananena kuti ngakhale kuti mliriwu ndi wodetsa nkhawa, ukupereka umboni wamphamvu wakuti “tili mbali yomalizira ya nthawi yamapetoyi. Kunena zoona, tili kumapeto a mapeto a masiku otsiriza.”

Ngakhale kuti masiku amene tikukhalawa ndi ovuta kwambiri, M’bale Lett ananena kuti: “Ifeyo monga atumiki a Yehova, sitikufunika kuchita mantha ngakhale pang’ono.”

Lipoti lililonse limakhala ndi nkhani zolimbikitsa zochokera m’mayiko osiyanasiyana padziko lonse. Malipoti amenewa amasonyeza kuti ndi nzeru kutsatira malangizo ochokera ku Bungwe Lolamulira. M’mayiko ambiri, akuluakulu a boma anayamikira abale ndi alongo chifukwa chochita zinthu mwamsanga komanso mwanzeru pa nthawi ya mliriwu.

Chikumbutso Chosaiwalika

Kwa zaka zambiri, a Mboni za Yehova akhala akukumana pamodzi chaka chilichonse kuti achite mwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye. Koma chaka chino m’madera ambiri kukumana pamodzi kunali kosatheka kapena kosaloledwa. Choncho anthu ambiri anangopeza zizindikiro za pa Chikumbutso zoti agwiritse ntchito pabanja lawo n’kumvetsera nkhani ya Chikumbutsoyo pogwiritsa ntchito vidiyokomfelensi.

M’madera ena, zinali zosatheka kugwiritsa ntchito vidiyokomfelensi. Chitsanzo ndi m’magawo a nthambi 11 za ku Africa. M’nthambi zimenezi anakonza zoti pulogalamu ya Chikumbutso iwulutsidwe pa TV kapena pawailesi. Zimenezi zinathandiza kuti ofalitsa oposa 407,000 komanso anthu ena osawerengeka amvetsere nawo pulogalamuyi.

Misonkhano ya pa TV ndi Pawailesi

Bungwe Lolamulira linavomereza kuti njira imene inagwiritsidwa ntchito pa Chikumbutso izigwiritsidwanso ntchito munthambi zina poulutsa misonkhano ya mpingo. Izi zathandiza kuti ofalitsa amene ali m’mayiko osauka azitha kumvetsera misonkhano mlungu uliwonse pawailesi kapena pa TV. Pofika pano, madera amene maofesi a nthambi okwana 23 amayang’anira akutsatira njira imeneyi ndipo ena ndi a ku Africa, Europe, North America ndi South America.

Makomiti Othandiza pa Ngozi Zogwa Mwadzidzidzi

Mliri wa COVID-19, wachititsa kuti abale ndi alongo ena azivutika kupeza zofunika pamoyo. Makomiti oposa 400 othandiza pa ngozi zogwa mwadzidzidzi akhazikitsidwa padziko lonse kuti azithandiza ofalitsa amene sangapeze chithandizo kumipingo kwawo. M’chaka cha utumiki cha 2020, Bungwe Lolamulira linavomereza kuti ndalama zoposa madola 18 miliyoni zigwiritsidwe ntchito pothandiza ofalitsa oposa 330,000 omwe akuvutika chifukwa cha mliri wa COVID-19.

Misonkhano Yochita Kujambula

Kwa nthawi yoyamba pulogalamu ya msonkhano wachigawo inali yochita kujambulidwa. Abale a m’Bungwe Lolamulira ndi owathandiza awo anakamba nkhani zonse zapamsonkhanowu zochita kujambulidwa ngati mavidiyo. Kenako mavidiyowa anamasuliridwa m’zinenero zoposa 500. Msonkhanowu unaikidwa pa jw.org ndi pa JW Library kuti anthu azionera ali otetezeka kunyumba kwawo.

Abale ndi Alongo Akuzunzidwabe

Kuwonjezera pa kuvutika ndi mliri wa COVID-19, abale ndi alongo m’mayiko osiyanasiyana akuzunzidwanso kwambiri.

Chaka chathachi, a Mboni za Yehova ku Russia akhala akuvutika chifukwa chakuti apolisi akhala akuchita chipikisheni m’nyumba zawo komanso kuwamanga mosatsatira malamulo. Panopa abale ndi alongo 42 ali m’ndende ku Russia ndipo ena awiri ali m’ndende ku Crimea. Kuchokera pamene Khoti Lalikulu Kwambiri la ku Russia linapereka chigamulo chake mu 2017, apolisi achita chipikisheni m’nyumba za abale zoposa 1,000.

Dziko la Eritrea ndi limene lamanga a Mboni ambiri, moti panopa latsekera m’ndende a Mboni okwana 52. Ena mwa abale amene ali m’ndende ndi a Paulos Eyasu, a Isaac Mogos, ndi a Negede Teklemariam. Abalewa anamangidwa chifukwa chokana usilikali pa 17 September 1994. Abale ndi alongo enanso okwana 26 akhala ali m’ndende kwa zaka zoposa 10.

Tikupitiriza kupempherera abale ndi alongo amene ali kundende kuti akhalebe olimba mtima. Koma tikudziwa kuti akuyesetsa kukhalabe okhulupirika pamene akupirira mayesero.​—Chivumbulutso 2:10.

Anapirirabe Mokhulupirika

M’chaka cha utumiki chapitachi, a Mboni za Yehova padziko lonse anasonyeza kuti ndi okhulupirika kwa Yehova m’njira zosiyanasiyana. Ankagwiritsa ntchito njira zina zolalikirira, anapeza njira zatsopano zolimbikitsirana komanso ankamvera malangizo ochokera ku Bungwe Lolamulira ndi kuboma.

Ntchito zonse zosonyeza kudzipereka kwa Mulungu zimene abale ndi alongo athu anachita zimasonyeza kuti amakonda kwambiri Mlengi wathu. Zimene anachitazi zidzawathandizanso kuti adzapirire mayesero akuluakulu amene akubwera kutsogoloku.​—Yakobo 1:2, 3.