Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

M’bale Miguel Silva ndi mkazi wake Mónica, akukambirana nkhani ya M’bale Konstantin Bazhenov imene awerenga pa gawo la Nkhani Zokhudza Mboni za Yehova

APRIL 9, 2021
NKHANI ZA PADZIKO LONSE

Nkhani za pa Gawo Lakuti Nkhani Zokhudza Mboni za Yehova Zikuthandiza Kulimbitsa Ubale Wathu Wapadziko Lonse

Nkhani za pa Gawo Lakuti Nkhani Zokhudza Mboni za Yehova Zikuthandiza Kulimbitsa Ubale Wathu Wapadziko Lonse

Nkhani za pa gawo lakuti Nkhani Zokhudza Mboni za Yehova zokhudza abale ndi alongo athu amene akuzunzidwa zimatithandiza kukhala opirira. Zimatithandizanso kuwadziwa bwino. Ndipo zomwe amafotokoza zokhudza zimene zikuchitika pa moyo wawo, zimatilimbitsa, kutithandiza kukhala ogwirizana komanso kutitsimikizira kuti ndi wosangalala ngakhale kuti akukumana ndi mavuto. Zimene abale ndi alongo ena akufotokoza m’munsimu, zikusonyeza mmene nkhani zimenezi zikuthandizira abale padziko lonse.

Tiziganizira Zimene Tingachite

Miguel Silva ndi mkazi wake Mónica, (omwe ali pamwambawo) ndi apainiya apadera ku Portugal. Mofanana ndi ena tonsefe, nawonso moyo wawo wasintha kwambiri chifukwa cha mliriwu. Kusintha kumeneku kukhoza kumatichititsa kukhala ndi nkhawa ndipo nthawi zina, kumamva kuti tatopa kwambiri. Komabe, banjali linalimbikitsidwa ndi lipoti la pa gawo lakuti Nkhani Zokhudza Mboni za Yehova la M’bale Konstantin Bazhenov. Ali m’ndende, M’bale Konstantin, ankafunitsitsa kuwerenga Baibulo koma sanathe kulipeza. Komabe iye sanabwerere m’mbuyo, m’malomwake anayamba kulemba mavesi onse amene ankawakumbukira n’kumawagwiritsa ntchito ngati Baibulo. Zimene anachitazi zinathandiza Miguel ndi Mónica kuphunzira kanthu kena kofunika kwambiri. Miguel anati: “M’malo moganizira kwambiri zimene tikulephera kuchita pa nthawi ya mliriwu, tinayamba kuganizira zimene tingakwanitse kuchita pa nthawi imene tikungokhala pakhomoyi.”

Kuwonjezera pamenepo, Miguel ndi Mónica anaganiza zowonjezera nthawi yowerenga Baibulo ndi kuganizira mozama zimene awerenga. Mónica anati: “Sitikukayikira kuti Yehova adzatithandiza kukumbukira zonse zimene tikuphunzira.” Miguel anawonjezera kuti, “Nkhani ya M’bale Bazhenov yatithandizanso kuona kuti nthawi imene tikungokhala pakhomo chifukwa cha mliriwu, tiione kukhala mwayi wathu wolimbikitsa ena, kuimbira Yehova mosangalala ndiponso kupemphera mochokera pansi pa mtima.”

N’zotheka Kusiya Kuopa Kuzunzidwa

Mlongo Christine Mouhima Etonde akuwerenga nkhani ya abale athu ku Russia imene ikufotokoza mmene akupiririra chizunzo

Mlongo Christine Mouhima Etonde, mpainiya wokhazikika ku Cameroon, ananena kuti kwa zaka zambiri, nkhani zofotokoza kuzunzidwa kwa abale ndi alongo zinkamuchititsa kukhala ndi mantha. Koma kenako anafotokoza zimene zinamuthandiza kusintha maganizo. Iye anati, “Kuwerenga nkhani za pa gawo la Nkhani Zokhudza Mboni za Yehova zokhudza abale ndi alongo amene akupirira chizunzo n’kumene kwandithandiza kusintha maganizo. Ndikamawerenga nkhani zofotokoza mmene abale akuonera chizunzo ndiponso mapemphero awo otchula zinthu mwachindunji, ndikaona abale ndi alongo amisinkhu yosiyanasiyana akumwetulira komanso kuona zimene akhala akuchita pokonzekera chizunzo, zandithandiza kuti ndiyesetse kumudziwa bwino Yehova. Panopa ndayamba kukonda kwambiri Yehova moti ndafika pomadziona ndikuzunzidwa koma osachita mantha. Ndikumadziona ndikusangalala, kupemphera ndiponso kuganizira za Yehova.”

Tizikhala Wokonzeka Kufotokoza Zimene Timakhulupirira

M’bale Iulian Nistor ndi mkazi wake Oana, akukambirana nkhani zimene awerenga pa gawo lakuti Nkhani Zokhudza Mboni za Yehova zokhudza abale athu omwe akufotokoza molimba mtima za chikhulupiriro chawo

M’bale Iulian Nistor ndi mkazi wake Oana a ku Romania, anakhudzika mtima ndi mmene M’bale Anatoliy Tokarev ankafotokozera zokhudza chikhulupiriro chake pamene anali m’khoti. Iye ankafotokoza mtima uli m’malo komanso mwaulemu ndipo anali wotsimikiza mtima kukhalabe wokhulupirika kwa Yehova. Chitsanzo cha m’baleyu chinathandiza Iulian ndi Oana kuganizira mmene angafotokozere zimene amakhulupirira m’khoti. Oana anati, “Pa kulambira kwa pabanja, tinkayerekezera kuti tili pamaso pa woweruza m’khoti ndipo tikufotokoza zimene timakhulupirira. Zinali zovuta kufotokoza momveka bwino komanso mwaulemu ngati mmene m’bale Anatoliy ankachitira. Titamaliza kulambira kwathu kwa pabanja, tinkangoona kuti tili pafupi ndi abale ndi alongo athu. Tinaonanso kufunika kokonzekereratu mmene tingafotokozere zimene timakhulupirira komanso chifukwa chake timasangalala kukhala a Mboni za Yehova.”

Mapemphero Athu Azikhala Ogwira Mtima

Mlongo Anna Ravoajarison wa ku Madagascar, akuwerenga nkhani zimene zangotuluka kumene pa gawo lakuti Nkhani Zokhudza Mboni za Yehova

Mlongo Anna Ravoajarison wa ku Madagascar, anaganiza zoonanso bwino mapemphero ake kuti azikhala ogwira mtima. Anna atawerenga nkhani ya M’bale Jovidon Bobojonov anati: “Nthawi zina ndikatanganidwa kwambiri ndi zochita za tsiku ndi tsiku, ndimaona kuti ndikamapemphera ndimangobwereza zomwezomwezo ngati sindinakhale ndi nthawi yoganizira zimene ndikufuna kumuuza Yehova.” Anna ataganizira kwambiri chitsanzo cha Jovidon, anayamba kumvetsa mmene iye ankamvera. Anna anadzifunsa kuti, “Zikanakhala kuti ineyo ndikuzunzidwa ngati mmene ankamuzunzira Jovidon, kodi ndikanakwanitsa kutchula zinthu mwachindunji m’pemphero ngati mmene iye anachitira? Zimenezi zandithandiza kuona kuti ndisanayambe kupemphera, ndi bwino ndizikhala ndi nthawi yoganizira zimene ndikufuna kuuza Yehova. Ndikuthokoza kwambiri chifukwa cha nkhani zimenezi.”

N’zotheka Kumawakonda Kwambiri Abale Athu

M’bale Ruben Catarino ndi mkazi wake Andreia, akuwerenga nkhani ya banja lina la ku Russia lomwe likuzengedwa mlandu chifukwa cha zimene amakhulupirira

M’bale Ruben Catarino ndi mkazi wake Andreia omwe ndi apainiya okhazikika ku Portugal, panopa akukonda kwambiri abale ndi alongo. Ruben anati: “M’mbuyomu timadziwa kuti m’mayiko ena abale ndi alongo athu akuzunzidwa, koma sitimawadziwa bwinobwino. Sitimadziwa kuti ndi otani, mmene zinthu zilili pa moyo wawo kapenanso mavuto amene akukumana nawo. Tikuthokoza chifukwa cha nkhani zimene zikumaikidwa pa gawo lakuti Nkhani Zokhudza Mboni za Yehova. Panopa tikutha kuwadziwa bwino. Tikhoza kuwatchula m’pemphero komanso kupempha Yehova kuti awathandize kupirira mavuto amene akukumana nawo. Nkhanizi zikutithandiza kuti tiziwakonda kwambiri abale athu ndiponso kudziwa kuti kuwapempherera n’kofunika kwambiri.”

Kuphunzira Patokha N’kofunika Kwambiri

Mlongo Cecilia Cardoso akugwiritsa ntchito nkhani za pa gawo lakuti Nkhani Zokhudza Mboni za Yehova ngati mbali ya pulogalamu yake yophunzira Baibulo payekha

Sitikukayikira kuti ambirife timamva mofanana ndi Mlongo Cecilia Cardoso yemwe ndi mpainiya wokhazikika ku Portugal. Iye anati: “Panopa ndikuona kuti kuphunzira pandekha n’kofunika kwambiri ndikaganizira zimene abale ndi alongo athu akukumana nazo. Ndikuona kuti kuphunzira Baibulo mozama n’kothandiza kuti ndizidalira Yehova ndiponso kumukonda kwambiri. Iye adzandithandza kuti ndisamachite mantha. Ndaphunzira kuti tikasiya kudalira Yehova, m’pamene timachita mantha komanso kuda nkhawa kwambiri.”

Tikuthokoza kwambiri chifukwa cha nkhani zimene zikumaikidwa pa webusaiti yathu zokhudza abale ndi alongo amene akupitirizabe kukhala okhulupirika komanso olimba mtima. Nkhanizi zikutithandiza kuti tikhale “olimba mtima” ndiponso kunena kuti ‘Yehova ndiye mthandizi wathu. Sitidzaopa.’—Aheberi 13:6.