Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

NOVEMBER 14, 2019
NKHANI ZA PADZIKO LONSE

Ntchito Yapadera Yolalikira Anthu Olankhula Chiarabu ku Austria ndi ku Germany

Ntchito Yapadera Yolalikira Anthu Olankhula Chiarabu ku Austria ndi ku Germany

Kuyambira pa 31 August mpaka pa 26 October, 2019, abale ndi alongo ochokera m’mayiko 19 anagwira nawo ntchito yophunzitsa anthu Baibulo m’gawo la anthu olankhula Chiarabu ku Austria ndi ku Germany. Pa nthawi imeneyi, a Mboni za Yehova okwana 1,782 analalikira kwa maola 40,724, anaonetsa mavidiyo athu maulendo 4,483, komanso anagawira mabuku othandiza pophunzira Baibulo okwana 24,769.

M’zaka zingapo zapitazi, anthu othawa kwawo oposa 1 miliyoni anapita ku Austria ndi ku Germany ndipo ambiri ndi ochokera m’mayiko omwe anthu ake amalankhula Chiarabu. Ambiri mwa anthuwa anali oti sanamvepo uthenga wotonthoza wochokera m’Baibulo. Abale ndi alongo ochokera ku Canada, United States, ndi m’mayiko osiyanasiyana ku Europe anagwira ntchitoyi limodzi ndi ofalitsa 1,108 omwe amatumikira m’gawo la anthu olankhula Chiarabu ku Austria ndi ku Germany. Abale ndi alongo onsewa anakafika m’zigawo 24 kuphatikizapo m’mizinda ikuluikulu monga Berlin, Cologne, Dresden, Frankfurt, Graz, Hamburg, ndi Vienna.

M’bale wina anati: “Ntchito yapaderayi inatilimbikitsa kwambiri ndipo tinali tisanaganizepo kuti ingatilimbikitse kwambiri chonchi. Abale omwe abwera kudzathandiza nawo ntchitoyi, atilimbikitsa kwambiri ndipo tikuthokoza kwambiri thandizo lawo. Tikuyamikira kwambiri chifukwa tinali ndi mwayi wogwira nawo ntchito yapaderayi.”

Mnyamata wina yemwe amachokera m’dziko la anthu olankhula Chiarabu anapezeka nawo pamsonkhano wa Mboni za Yehova ndipo anafunsa m’bale wina mosangalala kuti: “Kodi mukudziwa zimene mawu akuti mahabba amatanthauza m’Chijeremani?”

M’baleyo anayankha kuti, “Liebe (chikondi)!”

Mnyamatayo ananena kuti, “Eya, n’zimene ndaona anthu akusonyezana pamsonkhanowu lero. Munandikomera mtima kwambiri. Aliyense amandipatsa moni pochita kundigwira m’manja. Ndinaona anthu ochokera kumayiko osiyanasiyana akuchitirana zinthu mwaulemu. Zikanakhala kuti anthu onse amachitirana zimenezi, ndikukhulupirira kuti dziko lonse likanakhala labwino kwambiri!”

Ponena zokhudza a Mboni za Yehova, munthu winanso anati: “Mumaphunzitsidwa bwino mmene mungachitire zinthu ndi anthu ena mokoma mtima ndipo ndinu limodzi mwa magulu a anthu abwino kwambiri.”

Banja lina lochokera m’dziko la anthu olankhula Chiarabu koma linakhalapo ku Germany pafupifupi kwa chaka chimodzi, linaitanira abale kunyumba kwawo kuti akamwe tiyi. Abalewa atafotokoza za cholinga cha ulendo wawo, mayi wa m’banjalo anafunsa kuti, “Kodi ndinu a Mboni za Yehova?” Abalewo atavomera, mayiyo anayankha kuti: “Sindikukhulupirira! Ndakhala ndikufunafuna a Mboni za Yehova kwa miyezi ingapo. Mpaka ndinapita ku siteshoni ya sitima kukakufunafunani. Lero siinu mwabwera kwathunu! Mulungu ndi amene wakutumizani kuno.”

Yehova anadalitsa kwambiri khama la abale ndi alongo amene anagwira nawo ntchito yapaderayi polalikira uthenga wa m’Baibulo wopatsa chiyembekezo kwa “anthu a mitundu yonse.”—Mateyu 28:19.