Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Mlongo Mieko Yoshinari ku Japan akulemba ndemanga yake mu zilembo zikuluzikulu chifukwa ali ndi vuto la maso

APRIL 28, 2021
NKHANI ZA PADZIKO LONSE

Sukulu ya Utumiki Waupainiya Inachitika pa Vidiyokomfelensi Kwa Nthawi Yoyamba

Sukulu ya Utumiki Waupainiya Inachitika pa Vidiyokomfelensi Kwa Nthawi Yoyamba

Chifukwa cha mliri, Sukulu ya Utumiki Waupainiya ya chaka chautumiki cha 2021, inachitika padziko lonse pogwiritsa ntchito njira ya vidiyokomfelensi. Aka n’koyamba kuti sukuluyi ichitike pogwiritsa ntchito njira imeneyi. Pofuna kuyamikira zimene gulu la Yehova linachita kuti sukuluyi ichitike, wophunzira anayesetsa kuchita zonse zomwe angathe kuti adzapezekepo. Zimene anthu akufotokoza m’munsimu zikusonyeza mmene Yehova anathandizira apainiya kuti apezeke nawo pa sukuluyi ngakhale kuti anakumana ndi mavuto ndi zinthu zina zothetsa nzeru.

Mlongo Mieko Yoshinari wa ku Japan wakhala akuchita upainiya wokhazikika kwa zaka 30. (Onani chithunzi pamwambapa.) Ngakhale kuti amavutika kugwiritsa ntchito zipangizo zamakono komanso ali ndi vuto la maso, anayesetsa kuti achite nawo sukulu ya apainiyayi. Iye anati: “Mfundo zimene ndapeza pofufuza pa nthawi yokonzekera, ndinkazilemba mzilembo zikuluzikulu kuti ndisamavutike kuwerenga. Yehova wandilimbikitsa kwambiri ndi sukulu ya apainiya imeneyi.”

Mlongo Anita Kariuki amene amakhala m’tauni ya Thika, yomwe ili pafupi ndi mzinda wa Nairobi ku Kenya, amakonza anthu tsitsi kuti azipeza zofunika pa moyo kwinaku akuchita upainiya. Kuti apezeke pa sukuluyi, anafunika kutseka bizinezi yakeyi kwa wiki yonse. Iye anati: “Ndinangopemphera kwa Yehova kuti andithandize, kenako ine n’kumapitiriza utumiki wanga ” Ndiyeno kumapeto kwa wiki yoti wiki yamawa sukulu ikuyambika, anakwanitsa kupeza ndalama zokwanira kugulira zinthu zina zofunika. Komabe, Anita ankafunika ndalama zina zokwana madola 30 a ku America kuti agulirenso zinthu zina. Ngakhale zinali choncho, iye anatseka bizinezi yake n’kukayamba nawo sukulu. Ndiyeno Lachitatu atamaliza kuphunzira, munthu wina amene anali ndi ngongole ya Anitayo, anamuimbira foni kuti akufuna kumpatsa ndalama yake. Ndalamayo inali yokwanira ndendende imene Anita ankaifuna kuti agulire zinthu.

M’nyumba ya mlongo Laurenth Madrigales ku Yoro m’dziko la Honduras, munadzaza madzi komanso matope. Matopewo anali ambiri mpaka 1 mita kuchokera pansi. Izi zinachitika chifukwa cha mphepo yamkuntho yotchedwa Eta komanso lota imene inabweretsa mvula yamphamvu. Banja lawo linasamuka m’nyumbayi ndipo pafupifupi katundu wawo yense anawonongeka. Pa nthawiyi m’pamenenso mlongo Laurenth analandira kalata yoti akalowe sukulu ya apainiya. Iye anasangalala kwambiri, komabe anali ndi nkhawa kuti pamene sukuluyi izidzayamba adzakhala asanamalize kuyeretsa m’nyumba yawo. Mlongo Laurenth anati: “Tsiku lililonse tinkayamba ntchito m’mawa kwambiri ndipo tinkamaliza usiku. Tinachita zimenezi kwa masiku ambiri. Ndinkakhala wotopa kwambiri moti sindinkatha kukonzekera zakusukulu choncho ndinafotokozera abale kuti sindikwanitsa kuchita nawo sukuluyi.” Iye anapemphera kwa Yehova kumufotokozera mmene zinkamupwetekera mu mtima. Koma kutangotsala masiku ochepa kuti sukulu iyambike, anangodabwa kuona abale ochokera ku Komiti Yothandiza Pakachitika Ngozi Zadzidzidzi akubwera kudzawathandiza kuyeretsa m’nyumba mwawo. Izi zinathandiza kuti mlongoyu akhale ndi nthawi yokonzekera za ku sukulu ndipo anakwanitsa kuchita nawo sukuluyi ali m’nyumba mwawo.

Mlongo Laurenth Madrigales ku Honduras komanso nyumba yakwawo imene inawonongedwa ndi mvula yamkuntho, isanakonzedwe

M’bale Spencer Stash ndi mkazi wake Alexandra ndi apainiya okhazikika ku Cleveland, Ohio, ku United States. Sukulu ya apainiya isanayambike, bambo a M’bale Spencer, a Robert, omwenso mkazi wawo anamwalira, anagonekedwa m’chipatala. Izi zinachititsa banjali kuona kuti zikhala zovuta kuti akalowe nawo sukuluyi. Koma a Robert anawalimbikitsa kuti afunika asaphonye. N’zomvetsa chisoni kuti kutangotsala masiku awiri kuti sukulu iyambike bambowo anamwalira. Ngakhale kuti anali ndi chisoni chachikulu, M’bale Spencer ndi mkazi wake Alexandra anachita nawo sukuluyi ndipo anangophonya tsiku loyambirira lokha. Iwo anapemphera kwambiri kwa Yehova ndipo iye anawapatsa mphamvu zomwe ankafunikira kuti akwanitse kupezeka nawo pa sukuluyi. M’bale Spencer ananena kuti anali ndi mtendere wamumtima chifukwa anachita zimene bambo ake ankafuna. M’baleyu ananenanso kuti: “Tikuyembekezera mwachidwi kudzawafotokozera bambo kuti tinakwanitsa kukapezeka nawo pa sukuluyi komanso kudzawauza zinthu zina zimene tinaphunzira. Ophunzira anzathu komanso alangizi athu anatilimbikitsa kwambiri, zomwe ndi zimene tinkafunikira.”

Zaka 10 zapitazi, M’bale Jung Dae-sik wa ku South Korea wakhala ali ku nyumba yosamalira okalamba. M’baleyu amayenda pa njinga ya anthu olumala chifukwa anachita sitiroko. Iye ankafuna kulowa sukulu ya apainiya ya ulendo wapita, koma chifukwa cha matenda anangopita tsiku limodzi lokha. Koma atalandira kalata yomudziwitsa kuti alowa nawo sukulu imene idzachitike kudzera pa vidiyokomfelensi, anasangalala kwambiri. Iye anati: “Ndinathokoza kwambiri kuti sukuluyi idzachitika pogwiritsa ntchito vidiyokomfelensi ndipo ndinagwetsa misozi. Zikanakhala kuti sinachitike pogwiritsa ntchito njirayi, sizikanatheka kuti ndilowe nawo sukulu ya apainiya. Ndinasangalala kwambiri kuti ndinapezeka nawo pa sukuluyi.”

M’bale Jung Dae-sik ku Korea akuchita nawo sukulu ya apainiya ali ku nyumba yosamalira okalamba

M’bale Eddy El Bayeh ndi mkazi wake Cherise, apainiya okhazikika ku Australia

M’bale Eddy El Bayeh ndi mkazi wake Cherise, amakhala ku New South Wales, ku Australia. Cherise ananena kuti: “ndinkaona kuti sindikuchita utumiki mwakhama. Ndandanda yolowera mu utumiki ndinali nayo koma sindinkadziwa kuti ndingatani kuti ndiwonjezere changu muutumiki.” Chimene mlongo wathuyu ankafunikira ndi sukulu ya apainiya basi. Atalowa sukuluyi, anati: “Ndinazindikira kuti pali njira zambiri zimene ndingagwiritse ntchito kuti ndiwonjezere utumiki wanga ngakhale pa nthawi imene zinthu sizili bwino.”

Nayenso Eddy anafotokoza mmene sukuluyi inamulimbikitsira. Iye anati: “Sukuluyi inali ngati hagi yochokera kwa Wamphamvu Yonse. Zinali ngati iye akundisisita paphewapa mwachikondi n’kumandiuza kuti: ‘Tiye osabwerera m’mbuyo, ndili nawe limodzi, ndimakukonda komanso ndimakuganizira.’”

Pali ma kalasi ambiri amene achitike chaka chino pogwiritsa ntchito njira ya vidiyokomfelensi. N’zolimbikitsa kwambiri kuona kuti Yehova akupitiriza kuphunzitsa anthu ake ngakhale kuti pali mavuto ambiri amene akuchitika m’dzikoli. Izi zimatikumbutsa zimene Yobu ananena kuti: “Mulungutu amachita zinthu zapamwamba ndi mphamvu zake. Kodi mphunzitsi winanso ndani wofanana naye?”​—Yobu 36:22.

Zithunzi zili m’munsizi ndi za alangizi komanso ophunzira a m’mayiko osiyanasiyana amenenso apindula ndi sukulu ya apainiyayi yomwe inachitika pogwiritsa ntchito vidiyokomfelensi.

 

ARGENTINA: Ophunzira akuoneka pa vidiyokomfelensi akuchita chitsanzo cha ulaliki wamwamwayi m’basi

CAMEROON: M’bale Guy Leighton mlangizi wa sukulu ya apainiya ndiponso mmishonale amene wakhala akutumikira ku Cameroon kwa zaka 12, akuonetsa ophunzira chithunzi cha mipukutu ya ku nyanja yakufa pa phunziro lofotokoza zokhudza kumasulira Baibulo

GREECE: M’bale Takis Pantoulas, woyang’anira dera yemwe amatumikira mipingo ya m’chigawo chapakati ku Greece, akuphunzitsa pa sukulu ya apainiya

ITALY: Imodzi mwa makalasi a sukulu ya apainiya imene inachitika m’Chingelezi ku Italy

MEXICO: Ena mwa amene analowa nawo sukulu ya apainiya omwe anagwiritsa ntchito buku latsopano la chilankhulo cha Chitsotsilu chimene chimalankhulidwa makamaka m’dera la anthu a Chiapas. Imeneyi inalinso kalasi yoyamba kuchitika m’chilankhulo cha Chitsotsilu chimene anthu akumeneko amalankhula

SRI LANKA: M’bale Nishantha Gunawardana ndi mkazi wake Shiromala omwe ndi apainiya apadera, ali mkalasi

TANZANIA: M’bale William Bundala yemwe ndi mkulu ku Zanzibar wakhala pabwalo pamene Wi-Fi imagwira bwino