Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

7 JUNE 2023
NKHANI ZA PADZIKO LONSE

Tayambiranso Kukaona Malo ku Beteli

Tayambiranso Kukaona Malo ku Beteli

Pa 1 June 2023, anthu anayambiranso kukaona malo ku ma ofesi a nthambi ambiri padzikoli. Chifukwa cha mliri wa COVID-19, panali patadutsa zaka zoposa zitatu chisiyireni kuona malo ku Beteli. Tsikuli linali lapadera kwambiri kwa abale ndi alongo onse amene amatumikira pa Beteli padziko lonse komanso kwa alendo amene anabwera kudzaona malo.

Abale ndi alongo omwe ankaonetsa alendo malo akupereka moni mwansangala kwa alendo omwe abwera kudzaona malo ku Likulu la Dziko Lonse ku Warwick, New York, U.S.A.

Alendo akafika, atumiki apabeteli ankawalandira mosangalala powasonyeza zikwangwani, kuimba nyimbo, kumwetulira komanso kuwahaga. M’bale Ellis Bott yemwe anayamba kutumikira kulikulu la Mboni za Yehova ku Warwick, New York pa nthawi ya mliri, ananena kuti: “Zinali zosangalatsa kuona atumiki a pa Beteli ataimirira panja pa malo ofikira alendo atanyamula zikwangwani zolandirira alendo. Anthu ambiri ankagwetsa misozi yachisangalalo ndipo zimenezi zinandikumbutsa kuti Beteli ndi malo apadera kwambiri.” Mlongo Alexis Alexander yemwe amayendera ku Beteli kwa masiku ochepa anasangalala kwambiri kukhala m’gulu lolandira alendo, zomwe zinathandiza alendowa kumva kuti alandiridwa ndi manja awiri. Iye anati: “Zinalidi zosangalatsa kuona mmene abale amakondera Yehova ndi nyumba yake.”

A Mi-yeon Jo ndi mwana wawo wamwamuna wazaka 8, Yoon, akuona malo ku Beteli ya ku Korea

Mi-yeon Jo anasangalala kwambiri atapita ndi mwana wake Yoon wazaka 8 kukaona malo kunthambi ya ku South Korea. Yoon anasangalala kwambiri kuti akupita ku Beteli kokaona malo moti ankangoona kuchedwa kucha. Mi-yeon ananena kuti: “Titangodzuka, tinayamba kumvetsera nyimbo ya Kalebe ndi Sofiya atapita kukaona malo ku Beteli. Nyimboyi tinkaimvetsera mugalimoto tikupita ku Beteli.” Yoon anasangalala kwambiri ataona malo ndipo ananena kuti: “Pa Beteli pakufunikira zinyama, ndipo pangachite kukhala ngati paradaiso.”

Noah Johnsen ndi makolo ake akuona malo ku ofesi ya nthambi ya United States ku Wallkill, New York

Mnyamata wina wa ku Alberta, Canada dzina lake Noah Johnsen ali ndi vuto la msana ndipo ankafunitsitsa atakaona maofesi a nthambi ku New York, U.S.A. Popeza kuti sangathe kuyenda pandege chifukwa cha vuto lakeli, makolo ake anayenda naye pagalimoto mtunda wa makilomita 4,100 kuti akaone malo ku ofesi ya nthambi ya United States yomwe ili ku Wallkill, New York. Poganizira za ulendowu, Noah ananena kuti: “Zonse zimene zandichitikira pa ulendowu ndingaziike m’mawu amodzi akuti chikondi. Ndaoneratu kuti Yehova komanso abale ndi alongo amandikonda.”

A Fyodor Zhitnikov ndi akazi awo a Yulita, akuona myuziyamu ku ofesi ya nthambi ya ku Kazakhstan

A Fyodor Zhitnikov azaka 76 limodzi ndi akazi awo a Yulita anachita chidwi kwambiri ndi myuziyamu yomwe ili ku ofesi ya nthambi ya ku Kazakhstan. Mbali imodzi ya myuziyamu imeneyi imasonyeza nkhani za abale ndi alongo amene anapirira mokhulupirika kwa zaka zambiri. A Fyodor anaikonda kwambiri mbali imeneyi chifukwa anatumikirapo Yehova ndi ambiri mwa anthu amenewa. A Fyodor anayamikira kwambiri ntchito yomwe inagwirika pokonza mbali imeneyi. Iwo ananena kuti: “Ngati abale athu anaona kuti ndi bwino kusunga mbiri yokhudza utumiki ndi zochita za abale kwa zaka zonsezi ndiye kuti Yehova amakumbukira chilichonse komanso amayamikira ntchito imene wina aliyense amachita.”

Tikusangalala kuti panopa tikutha kulandiranso alendo ku nyumba zonse za Beteli padziko lonse. Tikuyembekezera mwachidwi kulandira anthu ankhaninkhani masiku akubwerawa.​—Salimo 122:1.

Chithunzi chili m’munsichi ndi cha abale ndi alongo athu amene anapita kukaona malo ku ma ofesi a nthambi osiyanasiyana komanso kumamyuziyamu.

 

Argentina

Belgium

Brazil

Dominican Republic

Ecuador

France

Kazakhstan

New Caledonia

Nigeria

South Korea

United States—Wallkill, New York

United States—Warwick, New York