Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

M’bale Sergey Filatov

MARCH 2, 2020
NKHANI ZA PADZIKO LONSE

Wa Mboni za Yehova Woyamba Kupezeka ndi Mlandu ku Crimea Akudikira Chigamulo cha Khoti

Wa Mboni za Yehova Woyamba Kupezeka ndi Mlandu ku Crimea Akudikira Chigamulo cha Khoti

Khoti la m’boma la Dzhankoysky ku Republic of Crimea likuyembekezera kulengeza chigamulo cha mlandu wa M’bale Sergey Filatov pa 5 March, 2020. Maloya anapempha khoti kuti M’baleyu akakhale m’ndende ya anthu opalamula milandu ikuluikulu kwa zaka 7. M’bale Filatov ndi wa Mboni woyamba kupezeka wolakwa ku Crimea mogwirizana ndi Buku la Malamulo a Zaupandu la ku Russia.

Monga mmene nkhani ina inanenerapo m’mbuyomu, Mbale Filatov anamangidwa pa nthawi imene apolisi a ku Russia anathyola n’kulowa m’nyumba 8 za a Mboni ku Crimea. Pa 10 October, 2017, gulu la abale ndi alongo linakumana kunyumba kwa M’bale Filatov kukakambirana mfundo za m’Baibulo ndi kuimba nyimbo za Ufumu. Nthumwi za apolisi a gulu loona za chitetezo ku Russia (FSB) zinkajambula mwachinsinsi zomwe ankakambirana pa msonkhanowo. Kenako madzulo a pa 16 November 2018, apolisi osachepera 200 anathyola ndi kulowa m’nyumba 8 za a Mboni za Yehova m’deralo. Akuluakulu oona za malamulo oposa 35 anakachita chipikisheni m’nyumba ya M’bale Filatov, ndipo pafupifupi hafu ya anthuwa anali asilikali onyamula zida. M’bale Filatov anafunsidwa mafunso kenako anamumasula.

M’bale Sergey Filatov, ndi mkazi wake Natalya ali ndi ana 4 ndipo awiri mwa anawa adakali ang’onoang’ono. Pamene M’bale Filatov akudikira chigamulo cha khoti, tikupemphera kuti iye limodzi ndi banja lake apitirize kudalira Yehova ndipo tikudziwa kuti Iye adzawathandiza pa nthawi ya masautsoyi.—Salimo 46:1.