Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Kumanzere: M’bale Yuriy Gerashchenko ndi mkazi wake, Irina. Kumanja: M’bale Sergey Parfenovich ndi mkazi wake, Marina

9 JANUARY 2024 | INAKONZEDWANSO PA: 3 JULY 2024
NKHANI ZA PADZIKO LONSE

ZOKHUDZA ABALE OMWE ANAPEZEDWA NDI MLANDU | Anatsimikiza Mtima Kuti Sasiya Kudalira Yehova

ZOKHUDZA ABALE OMWE ANAPEZEDWA NDI MLANDU | Anatsimikiza Mtima Kuti Sasiya Kudalira Yehova

Pa 1 July 2024, Khoti la m’Boma la Krasnogvardeyskiy ku Republic of Crimea linapeza kuti M’bale Yuriy Gerashchenko komanso M’bale Sergey Parfenovich ndi olakwa. Aliyense anagamulidwa kuti azitsatira malamulo enaake ali kunyumba kwawo kwa zaka 6 ndipo sakufunika kupita kundende panopa.

Zokhudza Abalewa

Tikudziwa kuti Yehova apitiriza kuthandiza Yuriy ndi Sergey kuti apitirizebe kukhala okhulupirika, pamene ‘akuwabisa mumthunzi wa mapiko ake.’​—Salimo 17:7, 8.

Nthawi Komanso Zimene Zinachitika

  1. 19 September 2022

    Mlandu wa Sergey unatsegulidwa

  2. 28 September 2022

    Apolisi agulu lachitetezo (FSB) anakafufuza kunyumba ya Sergey ndi nyumba zinanso 8 kenako anamutsekera kundende kwa nthawi yochepa

  3. 30 September 2022

    Sergey anaikidwa m’ndende poyembekezera kuzengedwa mlandu

  4. 15 November 2022

    Sergey anatulutsidwa m’ndende kenako anaikidwa pa ukaidi wosachoka panyumba

  5. 22 March 2023

    M’bale Yuriy anamutsegulira mlandu. Anamangidwa, kufunsidwa mafunso n’kuikidwa m’ndende kwa nthawi yochepa

  6. 24 March 2023

    Yuriy anatulutsidwa m’ndende kenako anaikidwa pa ukaidi wosachoka panyumba

  7. 12 July 2023

    Sergey ndi Yuriy anamasulidwa pa ukaidi wosachoka panyumba n’kuuzidwa kuti asamapite m’madera ena

  8. 28 July 2023

    Mlandu unayamba kuzengedwa. Loya woimira boma ananena kuti a Sergey ndi a Yuriy akupitiriza “kuchita zinthu zophwanya malamulo komanso kuopseza mboni za khoti.” Ngakhale kuti sipanapezeke umboni uliwonse, woweruza anagamula kuti onse akhalenso pa ukaidi wosachoka panyumba