20 JANUARY, 2022
NKHANI ZA PADZIKO LONSE
Zomwe Mungachite Kuti Muzigwiritsa Ntchito Bwino Buku la Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kale pa JW Library
Mu January 2021, Bungwe Lolamulira linalengeza za kutulutsidwa kwa buku komanso kabuku ka Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale. Mabukuwa komanso njira yophunzitsira anthu mochita kukambirana, zathandiza kuti tizitha kuphunzitsa anthu mwaluso kwambiri.
Pali zinthu zatsopano zomwe zawonjezeredwa mu apu ya JW Library kuti mphunzitsi komanso wophunzitsidwa azitha kugwiritsa ntchito mosavuta buku komanso kabuku ka pachipangizo chamakono. Pezani nthawi kuti muone mmene zinthu zatsopanozi zikugwirira ntchito.
Mukafuna kusonyeza wophunzira wanu mfundo ya m’phunziro lina lake, sankhani ndime imene mukufunayo, ndipo pabwera kabokosi kokhala ndi zinthu zosiyanasiyana zomwe mungasankhe. Kenako dinani Share kuti mutumizire wophunzira wanu linki ya ndimeyo.
Mukafuna kumvetsera mawu ojambulidwa a ndime inayake, sankhani ndimeyo, ndipo pabwera kabokosi kokhala ndi zinthu zosiyanasiyana zomwe mungasankhe. Kenako dinani pa Play kuti mumvetsere mawu a ndimeyo akuwerengedwa.
Tiyerekeze kuti mukugwiritsa ntchito buku la pachipangizo chamakono ndipo wophunzira wanu akugwiritsa ntchito buku lenileni lochita kupulinta, ndipo mukufuna kuona mmene buku lopulintalo limaonekera. Dinani pa More (pa timadontho titatu, pamwamba pakona yakumanja), n’kusankha pa Printed Edition. Mukafuna kubwerera, pitaninso patimadontho titatu tija, n’kusankha pa Digital Edition.
Mukafuna kuthandiza wophunzira wanu amene akugwiritsa ntchito buku la pachipangizo chamakono kuti azikumbukira mmene phunziro likuyendera, mulimbikitseni kugwiritsa ntchito timabokosi tolembamo tomwe tili m’phunziro lililonse, kuti alembe tsiku limene mwamaliza kuphunzira komanso zolinga zomwe ali nazo. Akhozanso kuchonga m’mabokosi omwe ali pambali yakuti “Chongani Machaputala Omwe Mwawerenga.”