Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

MARCH 30, 2017
NKHANI ZA PADZIKO LONSE

A Mboni za Yehova Akukonzekera Misonkhano Ikuluikulu M’chaka cha 2017

A Mboni za Yehova Akukonzekera Misonkhano Ikuluikulu M’chaka cha 2017

NEW YORK—A Mboni za Yehova akhala akuitanira anthu ku misonkhano ikuluikulu imene akhale nayo m’chaka cha 2017.

Lachiwiri pa 11 April, 2017, a Mboni padziko lonse adzakhala ndi Mwambo Wokumbukira Imfa ya Khristu womwenso umatchedwa Mgonero wa Ambuye. Mwambowu umachitika kamodzi pachaka ndipo anthu onse akuitanidwa kudzakhala nawo pamwambowu. A Mboni akugwira ntchito yapadera yoitanira anthu ku mwambowu yomwe inayamba Loweruka pa 18 March, 2017, ndipo idzatha pa 11 April, 2017. Iwo akuchita zimenezi pogwiritsa ntchito kapepala komwe kakusonyeza kumene mwambowu udzachitikire malinga ndi kuderalo. A Mboni amaona kuti mwambowu ndi wofunika kwambiri ndipo akuyesetsa kuitanira anthu ochuluka ku mwambowu.

Pambuyo pa Mwambo Wokumbukira Imfa ya Khristu, a Mboni adzakhalanso ndi nkhani yochokera m’Baibulo ya 30 minitsi ya mutu wakuti “Tingatani Kuti Tizikhala Amtendere M’dziko la Athu Okwiyali?” Nkhani imeneyi idzakambidwa pa 15 ndi 16 April, 2017 m’Nyumba za Ufumu zambiri za Mboni za Yehova padziko lonse.

Kuyambira pa 19 May, 2017, a Mboni za Yehova adzayamba kuchita msonkhano wa masiku atatu wa mutu wakuti “Musafooke!” Msonkhano umenewu udzayamba kuchitika m’dziko la United States ndipo kenako udzachitikanso m’madera osiyanasiyana padziko lonse mpaka kumayambiriro kwa chaka cha 2018. Kutatsala milungu itatu kuti msonkhano uliwonse uchitike, a Mboni adzagwira ntchito yoitanira anthu ku msonkhanowo n’cholinga chowafotokozera kumene msonkhanowo udzachitikire m’dera lawo.

Misonkhano ikuluikulu imeneyi, komanso ina ing’onoing’ono imene a Mboni za Yehova amakhala nayo, ndi yaulere. Ofalitsa nkhani omwe akufuna kudzafalitsa nkhani zokhudza misonkhanoyi, akhoza kufunsa ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova m’dziko lawo kuti awauze zimene angachite.

Lankhulani ndi:

David A. Semonian, Office of Public Information, +1-845-524-3000