Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

MARCH 20, 2014
NKHANI ZA PADZIKO LONSE

Bambo Guy H. Pierce, Omwe Anali M’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova, Amwalira

Bambo Guy H. Pierce, Omwe Anali M’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova, Amwalira

NEW YORK—Bambo Guy H. Pierce, omwe anali a m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova, anamwalira Lachiwiri pa March 18, ali ndi zaka 79. Iwo amwalirira kulikulu la dziko lonse la Mboni za Yehova ku Brooklyn, New York.

Bambo Pierce anagwirapo ntchito m’makomiti osiyanasiyana oyang’anira ntchito imene a Mboni za Yehova amagwira, kuphatikizapo ntchito yawo yophunzitsa Baibulo yomwe ikuchitika padziko lonse. Chifukwa cha maudindo amenewa, bambowa ankayenda maulendo ambirimbiri kuzungulira dziko lonse lapansi ndipo ankagwiritsa ntchito nthawiyi kumalimbikitsa a Mboni za Yehova anzawo. Ngakhale kuti ankatanganidwa chonchi, ankayesetsabe kupeza mpata wolimbikitsa kapena kupereka malangizo kwa ena. Ndipo anthu ankamasuka nawo chifukwa ankakonda tinthabwala komanso kumwetulira. Anzawo amene ankawadziwa bwino anafotokozanso kuti anthu a mitundu komanso zikhalidwe zosiyanasiyana ankawakonda kwambiri a Pierce. Pa mwambo wa anthu amene anamaliza maphunziro awo a ntchito yolalikira nthawi zonse, bambo Pierce anafotokoza mfundo imene iwowo ankaitsatira pa moyo wawo. Iwo anati: “Nthawi zonse muzionetsetsa kuti mukuyendera mfundo zabwino, komabe khalani ololera. Osakanyoza anthu amene ali m’gawo lanu chifukwa chakuti chikhalidwe chawo ndi chosiyana ndi chanu.”

Bambo Guy Hollis Pierce anabadwa pa November 6, 1934 ku Auburn, m’dera la California. Anabatizidwa kukhala wa Mboni za Yehova pa August 14, 1955, ali ndi zaka 20. Pa May 30, 1977, anakwatira a Penelope (Penny) Wong, omwenso ndi a Mboni za Yehova, ndipo anabereka ana angapo. Kenako Bambo ndi Mayi Pierce anayamba kugwira ntchito yophunzitsa ena Baibulo nthawi zonse. M’kupita kwa nthawi, Bambo Pierce anayamba utumiki woyendera mipingo ya Mboni za Yehova m’madera osiyanasiyana m’dziko la United States. Iwo ankalimbikitsa anthu m’mipingo ndiponso ankalimbikitsa anthu omwe ankagwira ntchito yophunzitsa ena Baibulo nthawi zonse. Mu 1997, banja la a Pierce linaitanidwa kuti likatumikire ku ofesi ya Mboni za Yehova ya United States. Pa October 2, 1999, Bambo Pierce anakhala m’gulu la anthu amene ali m’Bungwe Lolamulira.

Bambo Pierce anali tcheyamani pa msonkhano wa pachaka wa bungwe la Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania, womwe unachitika pa October 5 ndi 6, 2013. Anthu 1,413,676 a m’mayiko 31, anamvetsera msonkhanowu kumalo omwe unkachitikira, kapena kudzera pa vidiyo ya pa Intaneti. Ndipo webusaiti yovomerezeka ya a Mboni za Yehova inanena kuti aka kanali koyamba kuti anthu a Mboni ochuluka chonchi asonkhane pamodzi.

Bambo Pierce asiya mkazi wawo Penny, ana 6 ndiponso zidzukulu zambiri. A Mboni za Yehova padziko lonse sadzawaiwala a Pierce chifukwa bambowa ankaona kuti a Mboni onse anali a m’banja limodzi.

M’chikalata chimene anzawo a m’Bungwe Lolamulira analemba, anafotokoza kuti Bambo Pierce anali ndi “chikhulupiriro cholimba komanso ankayesetsa kutsatira malamulo a Yehova.” M’chikalatacho munalinso mawu akuti: “Tipitiriza kulimbikitsidwa pa zaka zikubwerazi tikamakumbukira mmene Bambo Pierce ankachitira zinthu molimba mtima komanso mokhulupirika.”

Lankhulani ndi:

Kuchokera m’mayiko ena: J. R. Brown, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000