Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

(Kumanzere) Zinthu zina zimene tingachite pofuna kudziteteza ku matenda zikuphatikizapo kuonetsetsa kuti malo amene timakonda kuwagwiragwira pakhomo pathu komanso ku Nyumba ya Ufumu ndi oyera ndiponso aukhondo nthawi zonse; (Pakati) M’madera ena okhudzidwa, ofalitsa angasankhe kugwiritsa ntchito njira zina zolalikirira, monga kulalikira kudzera patelefoni; (Kumanja) M’madera omwe mwabuka mliri, potengera ndi mmene zinthu zilili ku deralo, akulu akhoza kuthandiza ofalitsa kupeza misonkhano yongojambulidwa.

MARCH 3, 2020
NKHANI ZA PADZIKO LONSE

Mliri wa Koronavairasi Komanso Zimene Tingachite Kuti Tidziteteze

Mliri wa Koronavairasi Komanso Zimene Tingachite Kuti Tidziteteze

Tsiku lililonse, likulu la Mboni za Yehova padziko lonse likufufuza kuti lidziwe kumene kwafika mliri wachilendo wa kolonavairasi (womwe ukudziwika kuti COVID-19). Timadziwa kuti Baibulo linalosera kuti mliri ndi chizindikiro cha masiku otsiriza. (Luka 21:11) Pakabuka mliri wa matenda, ndi nzeru kutsatira malangizo a mmene tingadzitetezere komanso mmene tingatetezere ena.—Miyambo 22:3.

Mwina mungakonde kudziwa mmene zinthu zilili ndi abale komanso alongo athu amene ali m’madera omwe akhudzidwa ndi mliriwu. Mliri wa COVID-19 wachititsa kuti abale asinthe zinthu zina m’maofesi anthambi ndi m’mipingo ku Italy, Japan, South Korea, ndi mayiko ena. Mwachitsanzo, nthambi zina zasiya kaye kulola alendo odzaona malo kapenanso kulandira alendo ena omwe sakhala pabeteli. Ku mayiko amenewa boma likuletsa kuti anthu ambiri asamasonkhane malo amodzi ndipo zimenezi zapangitsa kuti ofesi ya nthambi iimitse misonkhano yadera. Komanso, m’madera ena mipingo yasintha dongosolo lolowera mu utumiki ndi misonkhano ya mpingo. Ngakhale kuti pali mavuto amenewa, abale ndi alongo athu akupitirizabe kulimbitsa moyo wawo wauzimu ndiponso kulimbikitsana.—Yuda 20, 21.

Zoterezi zikachitika, abale athu aona kuti kutsatira mfundo zotsatirazi n’kothandiza. Mfundozi zingathandizenso inuyo ndi banja lanu ngati m’dera lanu mungagwe mliri wa matenda enaake.

  • Musachite Phuma. Mliri ukagwa timafunika kukhala tcheru ndi kutsatira malangizo, komabe sitifunika kuchita zinthu mwaphuma chifukwa chakuti tili ndi mantha.—Miyambo 14:15; Yesaya 30:15.

  • Muzitsatira Malangizo Omwe Boma Likupereka. Nthawi zambiri boma limakhazikitsa malamulo kapena kuletsa anthu kuchita zinthu zina pofuna kupewa matenda. Zikatero, ndi bwino kumvera malangizowo ndi kuwatsatira.—Aroma 13:1.

  • Muzikhala Aukhondo. Muzisamba m’manja ndi sopo pafupipafupi kapenanso muzigwiritsa ntchito mankhwala ophera majelemusi m’manja. Malo amene timakonda kuwagwiragwira pakhomo pathu komanso ku Nyumba ya Ufumu azikhala oyera ndiponso aukhondo nthawi zonse. A zaumoyo amanena kuti pa nthawi ngati zimenezi sibwino kugwirana m’manja chifukwa matenda sachedwa kufalikira tikamagwirana m’manja. Ponena za mliri wa kolonavairasi, Bungwe Loona za Umoyo pa Dziko Lonse laperekanso malangizo ena.

  • Muzisonyeza Kuti Mumakonda Ena. Ngakhale kuti tonsefe timadziwa kuti misonkhano yampingo komanso kulowa muutumiki ndi kofunika kwambiri, ngati mukudwala, ndi bwino kukhala kaye kunyumba n’cholinga choti musafalitse matenda. Zimenezi zingasonyeze kuti mumakonda ena ndipo zingateteze abale ndi alongo athu kuphatikizaponso anzathu omwe si Mboni.—Mateyu 22:39.

  • Muzitsatira Zilizonse Zomwe Zasinthidwa Pampingo. M’madera omwe mwabuka mliri wa matenda, ofesi ya nthambi ingafunike kuimitsa kaye misonkhano yampingo, misonkhano ikuluikulu komanso misonkhano ina yapadera. Zimenezi n’zimene zachitika m’madera omwe akhudzidwa kwambiri ndi mliri wa COVID-19 monga m’zigawo zina za ku Italy, Japan, ndi South Korea. Potengera ndi mmene zinthu zilili ku deralo, akulu akhoza kuthandiza ofalitsa kupeza misonkhano yongojambulidwa kuti azionera ali m’nyumba zawo. Ofalitsa akhoza kumalalikira polankhulana ndi anthu pafoni, kutumiza mauthenga pogwiritsa ntchito foni, maimelo, kapena makalata.