Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

NOVEMBER 29, 2018
NKHANI ZA PADZIKO LONSE

Apolisi a ku Russia Anathyola N’kulowa M’nyumba 8 za a Mboni ku Crimea

Apolisi a ku Russia Anathyola N’kulowa M’nyumba 8 za a Mboni ku Crimea

Lachisanu madzulo pa 16 November, 2018, apolisi pafupifupi 200 a gulu lina loona za chitetezo ku Russia (Federal Security Service), anathyola n’kulowa m’nyumba 8 za a Mboni za Yehova ku Crimea.

Chifukwa cha mantha komanso kuda nkhawa kwambiri ndi zimene apolisi omwe amanyamula zida komanso ovala zobisa nkhope amachita, pothyola ndi kulowa m’nyumba za abale athu, a Mboni awiri anayamba kudwala matenda othamanga magazi ndipo anawatengera kuchipatala. N’zomvetsanso chisoni kuti mlongo wina yemwe anali woyembekezera anapititsa padera.

Pamene ankathyola n’kulowa m’nyumba za abale athu, apolisi anachitira nkhanza a Aleksandr Ursu omwe ali ndi zaka 78. Apolisiwo anakanikizira a Ursu kukhoma, kuwagwetsa pansi, kenako n’kuwamanga ndi unyolo. Kuwonjezera pamenepo, apolisiwo anapanikizanso a Mboni ambiri ndi mafunso.

Panopa, m’bale Sergey Filatov yekha (yemwe ali kumanja) ndi amene anamupeza ndi mlandu. A Filatov anawapeza ndi mlandu wochita zinthu zosemphana ndi Gawo 282.2 la m’Buku la Malamulo a Zaupandu a dziko la Russia, mbali yoyamba. Dziko la Russia likunena kuti dera la Crimea likuyeneranso kumatsatira zomwe zili m’gawoli. M’bale Filatov ndi azaka 47 ndipo ali ndi ana 4 komanso ndi wa Mboni woyamba kupezeka ndi mlandu ku Crimea pogwiritsa ntchito lamulo lolimbana ndi zinthu zoopsa la ku Russia.

Ngakhale kuti nkhani za kuthyoledwa kwa nyumba komanso kuzunzidwa ndi zodetsa nkhawa kwa abale athu, tikuyang’ana kwa Mulungu wathu Yehova molimba mtima, kuti atithandize m’masiku otsirizawa odzadza ndi mayesero.—Yesaya 41:10.