Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

MAY 4, 2016
NKHANI ZA PADZIKO LONSE

Misonkhano Yachigawo ya Mboni za Yehova ya  2016 Ikufotokoza za Kukhala Okhulupirika

Misonkhano Yachigawo ya Mboni za Yehova ya  2016 Ikufotokoza za Kukhala Okhulupirika

NEW YORK—A Mboni za Yehova akuitanira anthu onse ku Msonkhano Wachigawo wa chaka cha 2016 wamutu wakuti “Pitirizani Kukhala Okhulupirika kwa Yehova.” Misonkhano yoyambirira idzayamba Lachisanu pa 20 May m’dziko la United States. Msonkhanowu ndi waulere ndipo udzachitika padziko lonse.

Msonkhanowu, womwe udzakhale wamasiku atatu, udzakhala ndi nkhani 49 zomwe zidzatambasule mutu waukulu womwe ndi wokhudza “kukhala okhulupirika.” Kuonjezera pamenepo, a Mboni akonza mavidiyo 35 afupiafupi ogwirizana ndi nkhani za mu msonkhanowu komanso mavidiyo ena awiri otalikirapo omwe adzaonetsedwe Loweluka ndi Lamlungu. Komanso kwa masiku onse atatu, chigawo chilichonse chizidzayamba ndi vidiyo ya nyimbo.

Monga akhala akuchitira zaka zam’mbuyomu, a Mboni adzagawira timapepala toitanira anthu ku msonkhanowu. Mungathe kudziwa masiku ndi malo omwe kudzachitikire msonkhanowu m’dera lanu kudzera pawebusaiti ya jw.org. Atolankhani amene akufuna kudziwa zambiri angafunse ku maofesi a Mboni za Yehova omwe ali m’dera lawo. Angathenso kufunsa dzina la munthu amene angayankhule naye ngati akufuna kudzajambula kapena kudzalemba nkhani zokhudza msonkhanowu.

Bambo David A. Semonian, omwe amayankhula m’malo mwa Mboni za Yehova ku likulu lawo ku New York anati: “Timakhulupirira kuti anthu amakhala mabwenzi enieni ngati aliyense ali wokhulupirika kwa mnzake. Choncho msonkhano wachaka chino uli ndi nkhani zomwe zingathandize anthu kukhala pa ubwenzi wolimba ndi anzawo, anthu a m’banja lawo ndipo koposa zonse, kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu. Sitikukayikira kuti onse amene adzapezeke pa msonkhanowu adzasangalala kwambiri.”

Lankhulani ndi:

David A. Semonian, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000