SEPTEMBER 7, 2021
ECUADOR
Khoti Loona za Malamulo ku Ecuador Lagamula Kuti a Mboni za Yehova Ali ndi Ufulu Wolambira
Pa 24 August 2021, a Mboni za Yehova anawina mlandu wofunika kwambiri ku Ecuador. Khoti Loona za Malamulo linagamula kuti ufulu wolambira ukuphwanyidwa ku San Juan de Ilumán m’dera la Imbabura. Zimene khotili linagamula, zithandiza kuti anthu makamaka okhala m’midzi ya m’dzikolo azilambira mwaufulu komanso zithandiza makhoti a m’mayiko ena.
Mu 2014, akuluakulu a m’dera lina anakakamiza a Mboni za Yehova kuti asiye kumanga Nyumba ya Ufumu. Iwo analetsanso abale ndi alongo athu kuti asamasonkhane pamodzi kuti azilambira komanso kuti asamalalikire nyumba ndi nyumba. Abalewa anatengera nkhaniyi kukhoti. Komabe oweruza mlandu awiri omwe ankaweruza mlanduwu anapereka chigamulo chosakomera a Mboni za Yehova ndipo ananena kuti ufulu wawo sunaphwanyidwe.
Pambuyo poti ayesetsa kuchita zonse zomwe angathe kuti athetse vutoli, abalewa anatengera mlanduwu ku Khoti Loona za Malamulo, lomwe ndi khoti lalikulu kwambiri m’dzikoli. Khotili linanena kuti khoti laling’onolo linaphwanya ufulu wolambira wa a Mboni za Yehova. Atsogoleri a m’derali komanso oweruza anauzidwa kuti akakhale nawo pa maphunziro okhudza ufulu wachikhalidwe ndi chipembedzo. Komanso, atsogoleriwa anauzidwa kuti “azithandiza kuti anthu azipembedzo komanso zikhalidwe zosiyanasiyana azikhala mwamtendere ndipo azititeteza ntchito zachipembedzo makamaka” za a Mboni za Yehova.
A Philip Brumley, omwe amaimira Mboni za Yehova pa nkhani za malamulo, ananena kuti: “Malamulo amene anthu amakhala nawo m’midzi yawo amawathandiza kuti azitha kusunga chikhalidwe chawo, koma sizoyenera kugwiritsa ntchito malamulo amenewo monga chida chophwanyira ufulu wa nzika zina.”
A Mboni za Yehova a ku San Juan de Ilumán akuyamikira kwambiri chigamulo chomwe khotili linapereka.
Timasangalala kwambiri kuona umboni wakuti ‘dzanja la Yehova’ likuthandiza abale ndi alongo athu kupambana pa milandu yoteteza ufulu wawo wolambira.—Miyambo 21:1.