JUNE 24, 2019
ECUADOR
Zokhudza Msonkhano wa Mayiko wa 2019 Wakuti “Chikondi Sichitha,” ku Guayaquil, Ecuador
Masiku: 14 mpaka 16 June, 2019
Malo: Estadio Monumental Banco Pichincha ku Guayaquil, Ecuador
Zinenero: Chinenero Chamanja cha ku Ecuador, Chingelezi, Chisipanishi
Chiwerengero cha Osonkhana: 53,055
Chiwerengero cha Obatizidwa: 702
Chiwerengero cha Alendo Ochokera ku Mayiko Ena: 5,300
Nthambi Zoitanidwa: Argentina, Belgium, Bolivia, Central America, Colombia, Cuba, Kazakhstan, Korea, Moldova, Myanmar, Poland, Spain, United States
Zina Zomwe Zinachitika: Sitediyamu ya Estadio Monumental Banco Pichincha ndi ya timu ya mpira ya Barcelona ndipo pulezidenti wa timuyi, José Francisco Cevallos anati: “Sitinakumanepo ndi vuto lililonse pamisonkhano yanu ya zaka za m’mbuyomu komanso wa chaka chino. Umenewu ndi umboni wosonyeza kuti muli ndi khalidwe labwino komanso mumachita zinthu mwadongosolo pamisonkhano yanu yonse. Sizophweka kuyendetsa zinthu chonchi, koma nthawi zonse mumachita bwino ndiponso kukonzekera mokwanira misonkhano yanu yonse. Ndinu anthu abwino. Mumasonyeza khalidwe labwino, mumaphunzitsidwa bwino kwambiri, ndinu aulemu komanso adongosolo. Tikulimbikitsa akuluakulu onse a mizinda ndi mayiko kuti azilola a Mboni za Yehova kuchita misonkhano yawo.”
Alendo akujambulitsa pa nthawi yoona malo ku Beteli ya ku Ecuador
Abale ndi alongo a ku Ecuador ali muutumiki limodzi ndi alendo ochokera ku mayiko ena
Alendo ochokera kumayiko ena akuimba nyimbo pa tsiku loyamba la msonkhano
Ena mwa abale ndi alongo atsopano 702 akubatizidwa
Alendo akulemba notsi pamene nkhani zikukambidwa
Alendo akupanga chizindikiro chosonyeza chikondi chomwe anthu a ku Korea amapanga
M’bale Kenneth Cook wa m’Bungwe Lolamulira akukamba nkhani yomaliza pa tsiku Loweruka la msonkhano
Alendo omwe ali muutumiki wa nthawi zonse wapadera akubayibitsa anthu pa tsiku lomaliza la msonkhanowu
Abale ndi alongo a ku Ecuador akusangalatsa alendo madzulo pa nthawi yapadera