Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

7 JUNE, 2017
EGYPT

‘Ndikufunitsitsa Kudzaona Boma Litachotsa Chiletso Chomwe Linaikira a Mboni za Yehova’

‘Ndikufunitsitsa Kudzaona Boma Litachotsa Chiletso Chomwe Linaikira a Mboni za Yehova’

A Ehab Samir ndi a Mboni za Yehova ndipo ndi nzika ya ku Egypt. A Samir ali ndi zaka 52. Iwo anafotokoza kuti boma la Egypt linaletsa chipembedzo cha Mboni za Yehova ndipo linaika malamulo okhwima kwambiri. A Mboni ambiri amazunzidwa ndi akuluakulu a boma ndipo “amawaona ngati anthu ophwanya malamulo.” A Samir analimbikitsidwa atawerenga nkhani yokhudza a Mboni yomwe inaikidwa pawebusaiti inayake.

Nkhaniyo inali ndi mutu wakuti, “Dr. Riham Atef alemba nkhani yokhudza a Mboni za Yehova” ndipo inafalitsidwa pa 19 August, 2016. Nkhaniyi inafalitsidwa pawebusaiti ya Shbab Misr yomwe imafalitsa nkhani ku Egypt. Dr.  Atef ndi pulofesa payunivesite ya Cairo komanso ndi mtolankhani. Iwo anatsutsa nkhani zabodza zokhudza Mboni za Yehova zomwe anthu amanena ku Egypt. Mayi Atef amadziwana ndi anthu ena omwe ndi a Mboni za Yehova ndipo atafufuza bwino zokhudza a Mboniwo ananena kuti: “Ndimawadziwa bwino anthuwa ndipo amalemekeza zimene ena amakhulupirira.”

“Ndi Anthu Achikondi Komanso Okonda Mtendere”

Dr. Atef ananena za anthu omwe ankawalembera nkhaniyi kuti “sadziwa chilichonse chokhudza a Mboni za Yehova ndipo amangodana nawo chifukwa choti anthu ena anawanamiza.” Iwo anamaliza ndi kufotokoza zinthu zina zomwe a Mboni amakhulupirira ndipo anafotokozanso kuti “zambiri zokhudza a Mboni mungazipeze pawebusaiti yawo ya www.pr418.com.”

Atafufuza zambiri zokhudza a Mboni za Yehova, Dr. Atef anafotokoza zosiyana kwambiri ndi zimene anthu ambiri ku Egypt amaganiza. Iwo ananena kuti: “Sindimvetsa kuti n’chifukwa chiyani chipembedzochi anachitseka. Anthuwa salowerera nkhani zandale. Ndi anthu achikondi komanso okonda mtendere.” M’nkhaniyo Dr. Atef anafunsa kuti: “Kodi zifukwazi n’zomveka kuti mpaka n’kuwatsekera chipembedzo chawo? Kapena anawatsekera chifukwa choti zimene amakhulupirira kuchokera m’Baibulo n’zosiyana ndi ena?

‘Ndikufunitsitsa Kudzaona Boma Litachotsa Chiletso Chomwe Linaikira a Mboni za Yehova’

A Samir anasangalala kwambiri ndi nkhani yomwe Dr. Atef analemba yokhudza a Mboni moti sakanachitira mwina koma kulemba kalata yothokoza kwa mkonzi wa nyuziyi. A Samir ananena kuti: “Ndakhala ndikuwerenga nkhani za a Mboni za Yehova m’manyuzi a ku Egypt kuno, koma ndi nkhani zochepa chabe zomwe zimanena zoona zokhudza a Mboniwa. Ndikuthokoza kwambiri Dr. Riham Atef chifukwa chonena chilungamo komanso chifukwa cha kulimba mtima kwawo.” Kalata ya a Samir inaikidwanso m’nyuzi ya pa intanetiyi pa 11 December, 2016.

M’kalatayo, a Samir anasonyeza kukhumudwa kwawo chifukwa cha nkhanza komanso zinthu zopanda chilungamo zomwe a Mboni akukumana nazo. Ananenanso iwowo komanso a Mboni za Yehova ena akukumana ndi mavuto onsewa chifukwa cha nkhani zabodza zomwe atsogoleri azipembedzo akufalitsa. Iwo ananenanso kuti: “Mukafuna kudziwa munthu winawake, ndi bwino kukumana naye komanso kulankhula naye pamaso m’pamaso. Choncho ndikuthokoza kwambiri Dr. Riham Atef chifukwa cha nkhani yomwe analemba.”

A Samir anamaliza kalala yawo ndi mawu okhudzidwa akuti: “Ndikufunitsitsa kudzaona boma litachotsa chiletso chomwe linaikira a Mboni za Yehova kuti tidzakhale ndi ufulu wopembedza m’dzikoli.”

Kuyembekezera Nthawi Yomwe ku Egypt Kudzakhale Ufulu Wachipembedzo

Zaka zambirimbiri m’mbuyomo, a Mboni za Yehova ku Egypt ankapembedza mwaufulu ndipo chipembedzo chawo chinali m’kaundula wa boma. Koma mu 1960 boma linanena kuti a Mboni ndi osavomerezeka m’dzikolo ndipo anakana kuwapatsa ufulu ngati umene amapereka ku zipembedzo zina zachikhristu.

Kuchokera nthawi imeneyo a Mboni za Yehova akhalabe akuyesetsa kusonyeza kuti ndi nzika zachikondi komanso zokonda mtendere ngati mmene Dr. Atef ananenera. Ambiri akugwirizana ndi zomwe a Samir ananena ndipo akufuna kuti boma la Egypt lipatse a Mboni ufulu wawo wachipembedzo.