23 MARCH, 2022
EL SALVADOR
Mboni za Yehova za ku El Salvador Zikusangalala kuti Zakwanitsa Zaka 50 Zikudziwika ndi Boma
Pofika mu March 2022, Mboni za Yehova za ku El Salvador zinakwanitsa zaka 50 monga chipembedzo chodziwika ndi boma. Boma litatipatsa chilolezo kuti tiyambe kugwira ntchito ku El Salvador pa 27 March 1972, chiwerengero cha ofalitsa chinakwera mofulumira kwambiri kuchoka pa ofalitsa 2,524 mu 1972 kukafika pa 5,632 mu 1976. M’dzikoli panopa, muli ofalitsa opitirira 38,000 omwe akutumikira m’mipingo 662.
Amishonale athu anafika m’dzikoli mu 1945 ndipo anadzipereka kwambiri pogwira ntchito yolalikira. Panthawiyo, zinali zosavuta kulembetsa kuti akhale nzika zadzikolo. Mipingo inayamba kukhazikitsidwa ndipo ofesi ya nthambi inakhazikitsidwa mu May 1946.
Mu 1968, kunakhazikitsidwa lamulo latsopano lomwe linaletsa kuti amishonale asamakhale m’dzikolo kwa zaka zopitirira 5. Poona mmene zimenezi zikanakhudzira ntchito yolalikira, abale omwe ankatsogolera ntchito yathu, anaganiza zolembera kalata akuluakulu aboma.
Chakumapeto kwa 1971, akulu okwana 30 a ku El Salvador, anaitanidwa kuti akakumane ku ofesi ya nthambi kuti akakambirane za nkhaniyi. Mkatikati mwa zokambiranazo, M’bale Baltasar Perla, Sr., amene patapita nthawi anadzayamba kutumikira mu Komiti ya Nthambi, anapempha akulu onse omwe anafika pamsonkhanowo kuti amupatse ziphaso zawo zomwe anapatsidwa ndi boma. Kenako anauza abalewo kuti alemba kalata yopita kwa akuluakulu aboma ndipo mayina ndi ma adiresi a abalewo awalembanso mukalatayo.
M’bale Juan Antonio Flores, m’modzi wa akulu omwe analipo pamsonkhanowo, ananena kuti: “Kenako M’bale Perla, Sr., anatiuza kuti, chifukwa choti mayina ndi ma adiresi anu alembedwanso mukalatayi, ngati akuluakulu aboma atafuna kuletsa ntchito yathu, inuyo mukhala oyambirira kusakidwa komanso kumangidwa.” M’bale Perla, Sr., anapereka mwayi kwa aliyense amene anali ndi mantha kuti atenge chiphaso chake. Palibe aliyense amene ananena kuti amubwezere chiphaso chake. Mwamwayi, boma silinaletse ntchito yathu ndipo palibe aliyense amene anamangidwa.
Zonse zinayenda bwino ndipo Bungwe la Mboni za Yehova linalembedwa mukaundula waboma m’chaka chotsatira. Kuyambira nthawi imeneyo, amishonale anayambiranso kutenga chilolezo chokhaliratu m’dzikolo. Kuwonjezera apo, zinakhala zosavuta kuti ofesi ya nthambi iyambe kuitanitsa mabuku komanso kuti abale azitha kufotokoza kwa akuluakulu aboma kapenanso a m’masukulu chifukwa chake sitichita nawo zinthu zina.
Pa 26 April 1972, nyuzipepala yaboma inalemba za cholinga chachikulu cha bungwe lathuli kuti ndi: “Kulalikira za uthenga wa m’Baibulo komanso uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu ndi cholinga chofuna kuperekera umboni za dzina, mawu komanso ukulu wa Yehova Mulungu Wamphamvuyonse.”
Kwa zaka zonsezi, Mboni za Yehova za ku El Salvador zakhala zikuchitadi zinthu mogwirizana ndi mawu amenewa.—Yesaya 25:9.