Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

DECEMBER 4, 2020
ERITREA

A Mboni za Yehova 28 Atulutsidwa M’ndende ku Eritrea

A Mboni za Yehova 28 Atulutsidwa M’ndende ku Eritrea

Pa 4 December 2020, abale 26 ndi alongo awiri anatulutsidwa m’ndende ku Eritrea. Iwo anamangidwa chifukwa cha zimene amakhulupirira. Iwo akhala m’ndende kwa zaka pakati pa 5 mpaka 26. Pa nthawi yonseyi, abale ndi alongo onsewa anayesetsa kukhalabe okhulupirika kwa Yehova Mulungu. Tonsefe monga gulu la abale padziko lonse, tikusangalala kwambiri kumva za nkhani yabwino imeneyi. Pamene tikusangalala, sitikuiwalanso abale ndi alongo 24 omwe panopa adakali m’ndende ku Eritrea. Tipitirizabe kuwapempherera ndi mtima wathu wonse.—Machitidwe 12:5.