10 OCTOBER 2024
ERITREA
A Mboni za Yehova Ambiri Amangidwa ku Eritrea
Pa Anthu 23 Amene Amangidwa Palinso Mlongo Wazaka 85
Pa 27 September 2024, apolisi ku Eritrea anathyola n’kulowa m’nyumba ina imene a Mboni za Yehova ankachitiramo misonkhano yawo mwamtendere. Apolisi anamanga anthu 24, ndipo pa anthu amenewa pali abale 6, alongo 16 ndi ana awiri. Patapita masiku atatu apolisiwo anabwereranso ndipo anamanga mlongo wazaka 85 yemwe amakhala pa nyumba yomwe ankachitira misonkhanoyo. Kenako ana awiriwo anatulutsidwa ndipo akuluakulu 23 otsalawo anatumizidwa kundende ya Mai Serwa.
Pofika pano a Mboni za Yehova okwana 63 ndi amene ali m’ndende ku Eritrea, ndipo anthu 10 ndi a zaka zoposa 70. Koma palibe m’bale kapena mlongo wathu aliyense kuphatikizapo amene amangidwa posachedwapa yemwe wapezeka ndi mlandu kapena kupezeka wolakwa.
Kwa zaka zambiri, a Mboni za Yehova akhala akuzunzidwa ku Eritrea. Zaka 30 zapitazo, pa 25 October 1994, pulezidenti wa ku Eritrea anathetsa unzika wa a Mboni za Yehova onse omwe anabadwira m’dzikolo. Kungoyambira nthawi imeneyo, abale ndi alongo athu akhala akuzunzidwa kwambiri komanso kumangidwa popanda zifukwa zomveka.
Ndife achisoni komanso okhudzika kwambiri chifukwa cha zimenezi. Tikupitiriza ‘kukumbukira amene ali m’ndende’ powapempherera. Tikukhulupirira kuti Yehova apitiriza kulimbikitsa abale ndi alongo a ku Eritrea, kuwathandiza kupirira komanso kuwapatsa mphamvu.—Aheberi 13:3.