Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

M’bale Paulos Eyasu, M’bale Isaac Mogos, ndi M’bale Negede Teklemariam, amene akhala m’ndende ku Eritrea kuyambira pa 17 September, 1994

SEPTEMBER 17, 2019
ERITREA

Akhala M’ndende kwa Zaka 25 ku Eritrea

Akhala M’ndende kwa Zaka 25 ku Eritrea

Dziko la Eritrea lakhala likuzunza kwambiri a Mboni za Yehova m’zaka zaposachedwapa. Pofika pa 17 September, 2019, atatu mwa abale amene anamangidwa omwe mayina awo ndi Paulos Eyasu, Isaac Mogos, ndi Negede Teklemariam, akhala ali m’ndende kwa zaka 25. Kuwonjezera pamenepo, abale enanso 39 ndiponso alongo athu 10 ali m’ndende.

Abale ndi alongo athu onse omwe panopa ali m’ndende sanauzidwe mlandu womwe anapalamula, sanaonekere m’khoti, kapenanso kupatsidwa chilango, ndipo sakudziwa kuti adzatulutsidwa liti. Abale 4 anafera m’ndende, ndipo atatu anafa atatulutsidwa chifukwa choti ankakhala mozunzika kwambiri m’ndende.

Mchitidwe wozunza a Mboni ku Eritrea unakula kwambiri pa 25 October, 1994 patatha pafupifupi chaka ndi hafu kuchokera pamene dzikoli linasiya kulamuliridwa ndi dziko la Ethiopia n’kuyamba kudzilamulira lokha. Yemwe anali pulezidenti watsopano pa nthawiyo ananena kuti a Mboni za Yehova obadwira ku Eritrea sanalinso nzika za dzikolo chifukwa ankakana kuchita nawo zandale. Pulezidentiyo analandanso a Mboni maufulu osiyanasiyana amene anthu ena onse amakhala nawo. Mwachitsanzo, a Mboni za Yehova saloledwa kuti amalize maphunziro awo, kupanga bizinesi, kapena kupita kunja kwa dzikolo.

M’zaka zaposachedwapa, mabungwe odziwika bwino oona za ufulu wa anthu anasonyeza kuti ndi okhudzidwa kwambiri ndi zimene boma la Eritrea likuchita, ponyalanyaza mwadala mfundo zokhudza ufulu wachibadwidwe zimene mayiko ambiri anagwirizana kuti aziyendera. Umboni wa zimenezi ukuonekera pa zimene dzikoli likuchita ndi milandu yokhudza a Mboni anzathu. Dziko la Eritrea lasankha kusatsatira mfundo zimene linauzidwa ndi mabungwewa.

Onani: “LIPOTI LAPADERA: A Mboni za Yehova Akuzunzidwa ku Eritrea

Tipitiriza kudziwitsa akuluakulu a boma ndi ena amaudindo zokhudza mmene zinthu zilili ku Eritrea. Pamene abale ndi alongo athu akupitiriza kusonyeza chikhulupiriro cholimba komanso kupirira nkhanza zoopsa zimene akukumana nazo, tikudalira Yehova yemwe ndi Mthandizi komanso ‘thanthwe lawo lothawirako.’—Salimo 94:22.