Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

ERITREA

Mfundo Zachidule Zokhudza a Mboni ku Eritrea

Mfundo Zachidule Zokhudza a Mboni ku Eritrea

A Mboni za Yehova amazunzidwa kwambiri ku Eritrea. Boma la Eritrea lakhala likutsekera m’ndende, kuzunza, komanso kuvutitsa a Mboni za Yehova kungoyambira pamene dzikoli linakhala loima palokha mu 1993. Lamulo lomwe linaperekedwa ndi pulezidenti pa 25 October, 1994, linanena kuti zimene a Mboni za Yehova achita ku Eritrea pokana kuchita nawo zandale komanso kulowa usilikali, zikusonyeza kuti “adzichititsa kuti asakhalenso nzika za dziko la Eritrea.” Zimenezi zinachititsa kuti boma lichotsere a Mboni maufulu omwe anthu onse amakhala nawo.

A Mboni ambiri anathawa m’dzikoli chifukwa chozunzidwa komanso kukumana ndi mavuto kwa zaka zambiri. A Mboni omwe adakali m’dzikoli nthawi zonse amakhala mwamantha chifukwa akhoza kuchitidwa zachipongwe ndipo amayenera kukhala osamala kwambiri akamachita zinthu zokhudza chipembedzo chawo. Kwa zaka zambiri, akuluakulu a boma la Eritrea akhala akumanga komanso kutsekera m’ndende a Mboni ambiri. Ena anawamanga atakana ntchito yausilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira komanso ena chifukwa chochita misonkhano ya chipembedzo, chifukwa chouza ena zokhudza Baibulo, kapenanso pazifukwa zosadziwa bwino. Anthu omwe amatsekeredwa m’ndende akuphatikizapo amuna achikulire, akazi, ndipo nthawi zina ngakhalenso ana. Azibambo atatu a Mboni akhala ali m’ndende kwa zaka zoposa 20. Pa anthu onsewa palibe yemwe anaimbidwa mlandu n’kupatsidwa chigamulo.

Kuzunzidwa kwa a Mboni za Yehova ku Eritrea kwachititsa kuti mayiko osiyanasiyana achitepo kanthu. Akuluakulu a boma m’mayiko a ku Africa, Europe, komanso United States, analankhula ndi akuluakulu a boma la Eritrea za nkhaniyi, koma boma silinachite zambiri kuti lithandize a Mboni. A Mboni akhala akupempha akuluakulu a boma la Eritrea maulendo ambiri ku Asmara kuti akambirane nawo pofuna kuthetsa mavutowa, koma akuluakulu a bomawo amakana kukumana nawo.