Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

APRIL 17, 2020
FIJI

Mphepo Yamkuntho Yotchedwa Harold Yawononga Kwambiri Zilumba za ku Vanuatu ndi ku Fiji

Mphepo Yamkuntho Yotchedwa Harold Yawononga Kwambiri Zilumba za ku Vanuatu ndi ku Fiji

Pa 5 April 2020, mphepo yamkuntho yotchedwa Harold yomwe ndi yamphamvu kwambiri, inawomba kuzilumba za kumpoto kwa dziko la Vanuatu. Mphepoyi inawononga zinthu zambiri. Pofika pa 8 April, inakafikanso ku zigawo zina za kum’mwera chakum’mawa komanso kum’mwera chakumadzulo kwa zilumba za Fiji ndipo inawononganso kwambiri. N’zosangalatsa kuti malipoti omwe tinalandira anasonyeza kuti palibe m’bale kapena mlongo aliyense amene anavulala kapena kuphedwa ndi mphepoyi.

Ku Espiritu Santo, kumakhala ofalitsa pafupifupi 280 ndipo chimenechi ndi chilumba chachikulu kwambiri chomwe chili kumpoto kwa Vanuatu. Mphepoyi inawononganso kwambiri nyumba ndi mbewu zapachilumbachi, mofanana ndi mmene inachitira ndi zilumba zinanso zapafupi. Ku Fiji, katundu wa ofalitsa pafupifupi 260 anawonongeka kwambiri ndipo kulibe madzi okwanira, magetsi komanso chakudya chokwanira.

Nthambi ya ku Fiji ikuyang’anira ntchito yopereka thandizo kwa amene akhudzidwa. Panopa akulu akulimbikitsa abale ndi alongo okhudzidwa ndi mphepo yamkunthoyi. Ndife osangalala kuti abale athu omwe akhudzidwa akuthandizidwa kupeza zofunikira pa moyo komanso akulimbikitsidwa ndi mfundo za m’Baibulo.—Miyambo 17:17.