4 SEPTEMBER, 2017
FINLAND
A Mboni za Yehova Akutonthoza Anthu Omwe Anakhudzidwa ndi Zauchifwamba ku Turku, Finland
HELSINKI—Lachisanu masana pa 18 August, 2017, mlongo mmodzi anaphedwa ku Finland pa zauchifwamba zomwe cholinga chake chinali kupha azimayi. Chigawengachi chinaphanso mzimayi wina ndi kuvulaza anthu enanso 8. Zauchifwambazi zinachitikira pamsika wina ku Turku, mzinda womwe uli kumwera chakumadzulo kwa Finland. Zimenezi zitangochitika, oimira ofesi ya nthambi ya Finland, woyang’anira dera, komanso akulu anathandiza komanso kutonthoza anthu amene anakhudzidwa ndi zauchifwambazi.
A Veikko Leinonen, omwe amayankhula m’malo mwa ofesi ya nthambi ku Finland anati: “Zimene zachitikazi ndi zomvetsa chisoni komanso zoopsa kwambiri. Chimene chikutimvetsa chisoni kwambiri n’choti mlongo wathu yemwe anali mpainiya, anaphedwa pamene amapanga ulaliki wa m’malo opezeka anthu ambiri. Tikudziwa kuti ngakhale munthu atayesetsa kuchita zinthu mosamala, n’zosatheka kupeweratu kukumana ndi ‘zinthu zosayembekezereka,’ monga zachiwawa komanso zinthu zochititsa mantha. Komabe tikupitiriza kutonthoza abale athu, makamaka banja la mlongo amene anaphedwa. Pemphero lathu ndi loti Yehova apereke mtendere wa mumtima kwa anthu amene akuvutika chifukwa cha zimene zachitikazi. Tipitirizanso kuchita zonse zofunika n’cholinga choti tisalore kuti kuda nkhawa kwambiri kutilepheretse kupita patsogolo ndi ntchito yathu yolalikira.”—Mlaliki 9:11; Aroma 15:13; Afilipi 4:6, 7.
Ofesi ya nthambi inatumiza kalata ku mipingo yonse ya ku Finland pofuna kutonthoza komanso kulimbikitsa anthu mwauzimu. Ofesi ya nthambiyi inakonzanso msonkhano wapadera n’cholinga chofuna kulimbikitsa abale ndi alongo 135 omwe amagwira nawo ntchito yolalikira m’malo opezeka anthu ambiri ku Turku. Apainiya asonyeza kulimba mtima ndipo ndi ofunitsitsa kupitiriza kulalikira m’malo opezeka anthu ambiri.
Anthu ambiri okhala ku Turku asokonezeka kwambiri akaganizira kuti zauchifwambazi zachitikira ku Finland, dziko lomwe nthawi zambiri limaonedwa kuti ndi limodzi mwa mayiko osaopsa padziko lonse. Patangotha tsiku limodzi zauchifwambazi zitachitika, abale ndi alongo athu anatonthoza anthu ndi mfundo za m’Malemba pamene ankalalikira mu msika umene munachitika zauchifwambazo komanso kunyumba ndi nyumba ndipo ankamvetsera anthuwo mwachisoni.
Ofesi ya nthambi ku Finland ikuyamikira kwambiri ubale wa padziko lonse chifukwa cha mapemphero a abale ndi alongo komanso mauthenga olimbikitsa. (1 Petulo 2:17; 5:9) Koposa zonse, tikuyamikira Yehova “Mulungu amene amatipatsa mphamvu kuti tithe kupirira ndiponso amene amatitonthoza.”—Aroma 15:5.
Lankhulani ndi:
International: David A. Semonian, Office of Public Information, +1-845-524-3000
Finland: Veikko Leinonen, +358-400-453-020