Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

AUGUST 6, 2019
FRANCE

Ofesi ya Nthambi ya ku France Yatsegula Malo Atsopano Osungirako Mabaibulo Akale

Ofesi ya Nthambi ya ku France Yatsegula Malo Atsopano Osungirako Mabaibulo Akale

Pa 25 July, 2019, ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ya ku France inatsegula malo atsopano osungirako Mabaibulo akale. Ofesi ya nthambiyi ili m’tawuni ya Louviers yomwe ili pamtunda wa makilomita 100 kuchokera mumzinda wa Paris. Mutu wofotokoza za malowa ndi wakuti “Dzina la Mulungu M’Baibulo la Chifulenchi.”

Baibulo la Chifulenchi la Olivétan lomwe linapangidwa mu 1535

Malo osungira Mabaibulo akalewa ali ndi Mabaibulo ambiri a Chifulenchi omwe sapezekapezeka komanso omwe ndi ofunika kwambiri. Limodzi mwa Mabaibulo ofunika kwambiri ndi Baibulo la Chifulenchi lotchedwa Olivétan lomwe linapangidwa mu 1535. Baibuloli limadziwikanso kuti “La Bible de Serrières.” Baibulo la Olivétan ndi Baibulo loyamba lathunthu la Chipulotesitanti kumasuliridwa m’Chifulenchi. Komanso ndi Baibulo la Chifulenchi loyamba lomwe linamasuliridwa kuchokera ku ziyankhulo zoyambirira zomwe Baibulo linalembedwamo. Baibuloli linathandiza kwambiri pa ntchito yomasulira Mabaibulo enanso monga Baibulo la Chingelezi lotchedwa Matthew Bible lomwe linafalitsidwa mu 1537, Baibulo la Chingelezi lotchedwa Geneva Bible, komanso la Chifulenchi lotchedwa Geneva Bible. Mabaibulo enanso amene sapezekapezeka omwe ali kumalowa ndi Baibulo la Chifulenchi lotchedwa Jacques Lefèvre d’Étaples lomwe linatulutsidwa ulendo wachitatu mu 1541, Baibulo la Chilatini la mu 1541 lotchedwa Pentateuch ndi Baibulo la Chilatini la mu 1545 omwe anapangidwa ndi wosindikiza mabuku wa ku Paris dzina lake Robert Estienne, komanso Baibulo la Chifulenchi la mu 1557 lomwe linapangidwa ndi wosindikiza mabuku wa mumzinda wa Lyon dzina lake Jean de Tournes.

Baibulo la Chilatini la mu 1541 lotchedwa Pentateuch (m’mwamba kumanzere) komanso Baibulo la Chilatini la mu 1545 (pakati m’munsi) omwe anapangidwa ndi Robert Estienne, ndiponso Baibulo la Chifulenchi la mu 1557 lomwe linapangidwa ndi Jean de Tournes (m’mwamba kumanja). Miviyo ikulozera pamene pali dzina la Mulungu lakuti Yehova m’Mabaibulowa

Baibulo la Olivétan, la Chilatini lotchedwa Pentateuch ndi Baibulo la Chilatini omwe anapangidwa ndi Estienne, ndiponso Baibulo la Jean de Tournes, onsewa ali ndi dzina la Mulungu lakuti Yehova. Poyamba Mabaibulowa anaperekedwa ku Dipatimenti Yosunga Zinthu Zakale ku likulu lapadziko lonse la Mboni za Yehova lomwe lili ku Warwick, New York. Mabaibulo amenewa anawonjezera chiwerengero cha Mabaibulo ena omwe analipo kale ku ofesi ya nthambi ya ku France.

A Enrique Ford, omwe amatumikira m’Dipatimenti Yosunga Zinthu Zakale anati: “Malo atsopano osungirako Mabaibulo omwe ali ku ofesi yathu ku France, akufotokoza zokhudza mbiri yochititsa chidwi ya Baibulo la chinenero cha Chifulenchi. Komanso malowa akuthandiza anthu kudziwa malo osiyanasiyana m’Baibulo amene pamapezeka dzina la Mulungu lakuti Yehova. Tipitiriza kufufuza Mabaibulo ochititsa chidwi komanso omwe sapezekapezeka kuti tidzawaike m’malo athu osiyanasiyana osungirako zinthu zakale padziko lonse.”