AUGUST 8, 2019
FRANCE
Zokhudza Msonkhano Wamayiko wa 2019 Wakuti “Chikondi Sichitha,” ku Paris, France
Masiku: 2 mpaka 4 August, 2019
Malo: Parc des Expositions de Paris-Nord Villepinte ku Paris, France
Zinenero: Chingelezi, Chifulenchi, Chijeremani, Chiromaniya, Chirasha, Chisipanishi
Chiwerengero cha Osonkhana: 37,809
Chiwerengero cha Obatizidwa: 265
Chiwerengero cha Alendo Ochokera ku Mayiko Ena: 5,500
Nthambi Zoitanidwa: Britain, Canada, Central Europe, Chile, Côte dʹIvoire, Ecuador, Greece, Kazakhstan, Moldova, New Caledonia, Tahiti, United States, ndi Zambia
Zina Zomwe Zinachitika: Mmodzi mwa akuluakulu a malo omwe msonkhano unachitikira, ataona mzera wamagalimoto omwe amalephera kuyenda mofulumira chifukwa cha kuchulukana, anati: “Kodi anthu inu simupsa mtima? Pa nthawi ya msonkhano wa Mboni za Yehova, palibe amene ankaimba hutala, palibe amene ankachita zinthu mwaukali, palibe yemwe ankaoneka wokhumudwa, komanso palibe amene ankalowera anzake kutsogolo kwa mzera wamagalimoto.”
Munthu wina wogwira ntchito muhotela imene alendo omwe anapita kumsonkhanowu ankakhala anati: “Ndaonapo magulu ambiri, koma gulu lanuli ndi labwino kwambiri.Anthu akuoneka osangalala ndiponso zinthu zili bwino kwambiri pamalowa.”
Abale ndi alongo a ku France akulandira alendo pabwalo la ndege ku Paris
Abale ndi alongo akulalikira m’malo opezeka anthu ambiri ndipo nsanja yotchuka ya Eiffel Tower ikuonekera kutsogoloko
Abale ndi alongo akucheza panja pamalo a msonkhano
Banja likubatizidwa pa tsiku Loweruka
Alendo ochokera ku Tahiti akumvetsera msonkhano atavala zovala zachikhalidwe cha kwawo
M’bale Anthony Morris wa m’Bungwe Lolamulira akukamba nkhani yomaliza pa tsiku Loweruka
Alendo omwe ali muutumiki wa nthawi zonse wapadera akuoneka pasikirini pamene akubayibitsa anthu msonkhano utatha pa tsiku Lamlungu
M’bale akusonyeza alendo omwe akudzaona Beteli mmene amapangira zakudya zosiyanasiyana za ku France