JUNE 23, 2020
GEORGIA
Baibulo la Dziko Latsopano Lokonzedwanso Latulutsidwa M’Chijojiya
Lamlungu pa 21 June 2020, Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika linatulutsidwa m’chinenero cha Chijojiya pamsonkhano wapadera womwe unachitika kudzera pa vidiyokomfelensi. M’bale Geoffrey Jackson wa m’Bungwe Lolamulira ndi yemwe anakamba nkhani yongojambula yofotokoza za kutulutsidwa kwa Baibuloli. Anthu omwe anaonera msonkhanowu anali 19,521. Baibuloli litangotulutsidwa kumene linaikidwa pa jw.org kuti anthu apange dawunilodi pa zipangizo zamakono.
Ntchito yokonzanso Baibulo limeneli inatenga zaka 4. Mmodzi mwa anthu omwe anagwira nawo ntchito yomasulira anati: “Kulemba zinthu m’njira yosavuta kumathandiza kuti anthu amisinkhu yonse asamavutike kumvetsa zimene akuwerenga. Ndikuona kuti mabanja adzasangalala kwambiri kuphunzira pogwiritsa ntchito Baibulo limeneli.”
Womasulira winanso anati: “Cholinga chathu n’choti anthu onse azimvetsa Mawu a Mulungu bwinobwino kaya anapita patali ndi sukulu kapena ayi.”
Sitikukayikira kuti anthu onse omwe aziwerenga Baibulo lomasuliridwa molondola komanso lomveka bwino limeneli, aziyamikira Yehova chifukwa chowapatsa mphatso yabwino yomwe ikusonyeza kuti amawakonda.—Yakobo 1:17.