Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

A Mboni atatu a ku Georgia omwe avala zovala zachikhalidwe cha dzikolo akujambulitsa ndi alendo awiri omwe anapita kumsonkhanowu.

NOVEMBER 22, 2018
GEORGIA

Msonkhano Wapadera Woyamba Kuchitika Mumzinda wa Tbilisi ku Georgia

Msonkhano Wapadera Woyamba Kuchitika Mumzinda wa Tbilisi ku Georgia

Abale ndi alongo a ku Georgia analandira alendo ochokera m’mayiko 18 ku Msonkhano Wapadera wa mutu wakuti “Limbani Mtima,” womwe unachitikira ku Tbilisi kuyambira pa 20 mpaka 22 July, 2018. Aka kanali koyamba kuti ku Georgia kuchitike msonkhano wapaderawu ndipo anthu anasangalala ndi nkhani zolimbikitsa zochokera m’Baibulo, kucherezana, magule ndi zinthu zina za m’deralo komanso mbiri ya dzikolo.

Msonkhanowu umachitikira ku sitediyamu ya Olympic Palace yomwe ili ku Tbilisi, ndipo chiwerengero chachikulu cha anthu omwe anasonkhana chinali 7,002. Ndipo anthu enanso anamvetsera nkhani za msonkhanowu kudzera pa Intaneti ali m’madera pafupifupi 80, zomwe zinachititsa kuti chiwerengero chonse cha osonkhana chikhale choposa 21,500. Chosangalatsanso kwambiri n’choti pamsonkhanowu abale ndi alongo atsopano okwana 208 anabatizidwa.

Kuwonjezera apo, abale ndi alongo ochokera kumayiko ena anasangalala kwambiri kuonera zinthu zosiyanasiyana za chikhalidwe cha anthu a ku Georgia. Abale ndi alongo a m’dzikoli anavina magule, kuimba nyimbo, kuphikira alendowa zakudya zosiyanasiyana za anthu a m’dzikoli komanso kuwaonetsa malo a mumzinda wakale wa Tbilisi.

A Tamaz Khutsishvili omwe anayankhula m’malo mwa ofesi ya nthambi ku Georgia anati: “Nthawi inayake m’mbuyomu tinalibe ufulu wolambira m’dziko lathuli. Koma ulendo uno akuluakulu a boma anatilola kuti tipange msonkhanowu mwamtendere chonchi, sitidzaiwala mwayi wapadera womwe tinali nawo wolandira abale ndi alongo athu ambirimbiri kuti adzakhale nafe pamsonkhano wosangalatsawu.”—Aroma 15:7.

 

Chiwerengero chapamwamba cha anthu 7,002 ndi omwe anapezeka pamsonkhano wapadera umene unachitikira pa Olympic Palace kuyambira pa 20 mpaka pa 22 July, 2018. Anthu enanso 14,912 anasangalala kuonera msonkhanowu pamasikirini m’malo osiyanasiyana m’dziko lonselo..

M’bale Stephen Lett yemwe ndi wa m’Bungwe Lolamulira, ankakamba nkhani yomaliza tsiku lililonse.

Nthawi yapadera kwambiri pamsonkhanowu inali pamene abale ndi alongo 208 anabatizidwa. Damu la ubatizoli linaikidwa pafupi ndi khoma la mwala wachilengedwe lomwe ndi mbali ya m’kati mwa Olympic Palace.

Anthu ankatha kuonera msonkhanowu m’malo osiyanasiyana okwana 80.

Alongo a ku Georgia akulandira mlendo yemwe anapita kumsonkhanowu. Mlongo mmodzi wavala chisoti chopangidwa ndi ubweya wa nkhosa ndipo chisotichi chimakonda kuvalidwa m’madera a mapiri a ku Georgia.

Mwambo wosangalatsa unachitika pa 17 ndi 18 July ku Château Mukhrani, komwe ndi m’mudzi wa Mukhrani pafupi ndi Tbilisi. Pamwambowo panaimbidwa nyimbo zachikhalidwe za ku Georgia komanso kuvina, ndiponso panawonetsedwa mavidiyo awiri ofotokoza mbiri ya choonadi ku Georgia.

A Mboni a ku Georgia akuvina gule wotchedwa Adjaruli (dzinali linatengedwa ku dzina loti Adjara, chomwe ndi chigawo china chimene chili kumpoto chakumadzulo kwa dziko la Georgia, pafupi ndi Black Sea). Guleyu amamukometsera ndi zovala zowala za m’derali.

Abale a ku Georgia akuimba nyimbo yachikhalidwe m’njira motsatira mmene anthu ankaimbira kalekale.