Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

GEORGIA

Mfundo Zachidule Zokhudza a Mboni ku Georgia

Mfundo Zachidule Zokhudza a Mboni ku Georgia

A Mboni za Yehova anayamba kugwira ntchito zawo ku Georgia kuyambira mu 1953. Iwo analembetsa ku boma monga chipembedzo chovomerezeka ndipo tingati amalambira Mulungu popanda chovuta. Komabe, pali mavuto ena omwe akupitirirabe, chifukwa choti m’dzikoli nthawi zina pamakhala kusalolerana pa nkhani zachipembedzo.

Kuyambira mu 1999 mpaka mu 2003, magulu achiwawa achipembedzo anayambitsa mchitidwe wochitira nkhanza a Mboni za Yehova. Anthuwo ankapitirizabe kuchitira nkhanza a Mboni chifukwa akuluakulu azamalamulo ankakana kuwapatsa chilango. Pa nthawi imeneyo, phungu wina wa nyumba ya malamulo yemwe amakonda kwambiri dziko lake, anachititsa kuti kwa kanthawi mabungwe ovomerezeka a Mboni asakhalenso ovomerezeka ndipo zimenezi zinachititsa kuti anthu apitirizebe kuchitira a Mboni zachiwawa. A Mboni anapereka madandaulo okwana 6 ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe kuti lithetse mavutowa. Mu 2007 komanso mu 2014, khotili linapereka zigamulo ziwiri zomwe oweruza onse anagwirizana nazo zodzudzula boma chifukwa cholephera kuthandizapo mwamsanga, kuchita zinthu zothandizadi kuti nkhanzazi zithe, komanso chifukwa cholephera kuchita zinthu mosakondera. Mu 2015, khotili linagwirizana ndi zomwe boma la Georgia linanena kuti linachotsa mopanda chilungamo a Mboni m’kaundula wake wa mabungwe ovomerezeka ndi boma mu 2001.

Kuyambira mu 2004, zachiwawa zomwe a Mboni za Yehova akhala akuchitidwa zachepako. Iwo akwanitsa kuwonjezera ntchito zawo komanso kumanga Nyumba za Ufumu zochuluka. Ngakhale zili choncho, nthawi zina amachitidwa zankhanza komanso amazunzidwa ndi magulu azipembedzo zina. Vutoli limawonjezeka chifukwa choti akuluakulu a boma nthawi zambiri amalephera kuthandizapo. A Mboni akuyembekezera kuti boma la Georgia litsatira zonse zimene Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Europe linagamula kuti lifufuze mwansanga zachiwawa zomwe a Mboni anachitidwa ndiponso anthu omwe anachita zimenezi aimbidwe mlandu.