Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

23 DECEMBER, 2021
GERMANY

Mabuku a Mateyu ndi Yohane Atulutsidwa M’chilankhulo Chamanja cha ku Germany

Mabuku a Mateyu ndi Yohane Atulutsidwa M’chilankhulo Chamanja cha ku Germany

Pa 18 December 2021, M’bale Dirk Grundmann wa mu Komiti ya Nthambi ya Central Europe, anatulutsa zigawo zoyambirira za Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika m’chilankhulo chamanja cha ku Germany. Anthu pafupifupi 800 anaonerera kutulutsidwa kwa mabuku a m’Baibulo a Mateyu ndi Yohane kudzera pa intaneti.

Boma la Germany linavomereza Chinenero Chamanja cha ku Germany monga chilankhulo choima pachoka, mu 2002. Komabe, a Mboni za Yehova akhala akutulutsa zinthu za m’chilankhulochi pamisonkhano yadera ndi yachigawo kuyambira m’zaka za m’ma 1960. Pofika pano, ofalitsa 571 akutumikira m’mipingo 11 ndi magulu 21 a Chinenero Chamanja cha ku Germany.

M’bale akumasulira nkhani m’chilankhulo chamanja pa msonkhano wachigawo ku Munich, Germany, mu 1973

Kameneka ndi koyamba kuti mabuku athunthu a m’Baibulo amasuliridwe m’chilankhulochi. M’mbuyomu, ofalitsa akamaphunzira paokha komanso akakhala muutumiki, ankangogwiritsa ntchito mavesi ochepa omwe anamasuliridwa.

Wofalitsa wina ananena kuti: “Chifukwa choti tinalibe Baibulo lathunthu ndipo tinkangodalira mavesi ochepa omwe anamasuliridwa, zinkakhala zovuta kumvetsa bwino mfundo za m’Baibulo komanso kufotokozera anthu chifukwa chake timakhulupirira zinazake.” Iye anapitiriza kunena kuti: “Zinkakhalanso zovuta kulimbikitsa munthu amene ukuphunzira naye kuti aziwerenga Baibulo tsiku lililonse chifukwa panali mavesi owerengeka chabe a m’Baibulo.”

Timu yomasulira Chinenero Chamanja cha ku Germany ikujambula vidiyo musitudiyo

Munthu wina amene anagwira nawo ntchito yomasulira Baibuloli anati: “Ndi zosangalatsa kwambiri kugwira nawo ntchito yomasulira Mawu a Yehova ndi cholinga chothandiza anthu a vuto losamva kuti akhale pa ubwenzi ndi Mulungu. Tasangalala kwambiri kupatsidwa mwayi wogwira nawo ntchito imeneyi.”

Ndi pemphero lathu kuti Baibulo la Dziko Latsopano la M’chilankhulo cha Manja cha ku Germany lithandiza anthu ambiri omwe ndi ofatsa kuti adziwe njira za Yehova.—Salimo 25:9.