FEBRUARY 22, 2021
GERMANY
Nyumba ya Malamulo ya ku Germany Inachita Mwambo Wokumbukira a Mboni za Yehova Chifukwa Cholimba Mtima Pozunzidwa ndi a Nazi
Pa 27 January 2021, Nyumba ya Malamulo ya ku Baden-Württemberg ku Germany, inakumbukira a Mboni za Yehova pa tsiku limene Nyumbayi imachita mwambo wawo wapachaka, wokumbukira anthu amene anachitiridwa nkhanza ndi chipani cha Nazi pa nthawi ya nkhondo yachiwiri ya padziko lonse. Chifukwa cha mliri wa COVID-19 mwambowu unachitikira pa intaneti. Anthu oposa 37,000 ochokera ku Austria, Germany, Netherlands ndi Switzerland anachita nawo mwambowu. Pulogalamuyi inajambulidwa n’kuikidwa pa intaneti ndipo inaoneredwa nthawi pafupifupi 78,000.
A Muhterem Aras omwe ndi pulezidenti wa Nyumba ya Malamulo ya Baden-Württemberg, anafotokoza kuti “tili ndi mabuku komanso zinthu zambiri zofotokoza mmene a Mboni za Yehova anazunzidwira, . . . koma ndi anthu ochepa amene amafotokoza bwino nkhani yonse.” Anafotokozanso kuti pa nthawi yovuta imeneyo, a Mboni za Yehova anasonyeza “chitsanzo chabwino chimene ifeyo tingatengere anthu ena akamadana nafe, akamatisala komanso mmene tingapewere zachiwawa.”
A pulezidenti a ku Nyumba ya Malamulo a Aras anafotokoza nkhani ya Mlongo Anna Denz, yemwe ankakhala ku Lörrach, ku Baden-Württemberg. Makolo a mlongoyu anamwalira ali kundende zozunzirako anthu. Anna ali kusukulu anakana kunena kuti “Hitler Mpulumutsi Wathu.” Pasanapite nthawi, iye anathawira ku Switzerland mothandizidwa ndi a Mboni anzake. Kenako Anna limodzi ndi mwamuna wake anathawira ku United States. Pulezidentiyu ananenanso kuti “Anna Denz anakwanitsa kupirira, chifukwa chakuti anali ndi chikhulupiriro cholimba.”
Dr. Hans Hesse yemwe ndi katswiri wa mbiri yakale, anafotokoza kuti a Mboni za Yehova ku Germany analetsedwa mu 1933, patangotha miyezi iwiri kuchokera pamene chipani cha Nazi chinayamba kulamulira. Dr. Hesse anafotokozera anthu amene ankamvetsera kuti, a Mboni “sanamvere za chiletsocho ndipo ankapitiriza kugawira timapepala kapena kulalikira.”
Katswiri wolemba mbiriyu anafotokozanso nkhani ya M’bale Gustaf Stange. M’bale Stange ali kukhoti pa mlandu wokana kulowa usilikali chifukwa cha chikhulupiriro chake, wozenga mlandu anafunsa kuti: “Kodi chingachitike n’chiyani ngati aliyense atachita zimene ukuchita iwezi?” M’bale wathuyu anayankha kuti: “Ndiye kuti nkhondo ikhoza kutha nthawi yomweyo.”
Pamwambo wa pa intanetiwu anaikanso nyimbo ya Ufumu yakuti, “Pitani Patsogolo Mboninu.” M’bale Wolfram Slupina, yemwe amayang’anira Dipatimenti Yoona Zofalitsa Nkhani ku ofesi ya nthambi ya ku Central Europe ananena kuti, M’bale Erich Frost yemwe anali katswiri woimba, ndi amene anapeka mawu oyambirira a munyimboyi pamene anali kundende yozunzirako anthu ya Sachsenhausen mu 1942. Zaka zambiri m’mbuyomu M’bale Frost akufunsidwa mafunso, anafotokoza kuti cholinga cha nyimboyi chinali kulimbikitsa akaidi anzake chifukwa pa nthawiyi “kundendeko ankazunzidwa kwambiri.”
Mara ndi Finn Kemper, a zaka 13 ndi 15, omwe ndi a Mboni za Yehova, anafunsa mafunso Mlongo Simone Arnold Liebster, yemwe anapulumuka nkhanza za chipani cha Nazi. Mlongo Liebster ali mwana anapirira pamene ankatsutsidwa kwambiri. Chifukwa chakuti anakana kulowa m’chipani cha Nazi, akuluakulu a chipanichi anamutumiza kundende ya ana. Iye ananena kuti kundendeko “ankakhalabe wosangalala” chifukwa anali wokhulupirika ngakhale pamene ankazunzidwa.
Ndife osangalala kuti mwambo umenewu unapereka umboni wamphamvu wokhudza Yehova kwa anthu ambiri. Yehova anasonyeza kuti amathandiza anthu ake ngakhale pamene akuzunzidwa kwambiri.—Aheberi 13:6.