Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

MAY 1, 2013
GERMANY

Dziko la Germany Lapereka Mendulo Yaulemu kwa Mayi Wina wa Mboni za Yehova Poyamikira Ntchito Yake Yotamandika

Dziko la Germany Lapereka Mendulo Yaulemu kwa Mayi Wina wa Mboni za Yehova Poyamikira Ntchito Yake Yotamandika

SELTERS, Germany​—Pa February 22, 2013, mayi wina wa Mboni za Yehova dzina lawo a Mathilde Hartl analandira mendulo yapadera. A Horst Seehofer, omwe ndi nduna yaikulu ya chigawo cha Bavaria ndi amene anapereka mendulo imeneyi. Boma la Germany limapereka mendulo imeneyi kwa anthu okhawo amene achita zinthu zazikulu m’dzikolo.

Mayi Hartl amene amakhala m’chigawo cha Bavaria anapatsidwa mendulo imeneyi chifukwa cha zimene anachita posamalira kwa nthawi yaitali mwana wawo wamwamuna wolumala dzina lake Martin. Mwanayu panopa ali ndi zaka 26. Pamene Martin anali wamng’ono anapezeka ndi matenda enaake (Duchenne muscular dystrophy [DMD]) amene amagwira minofu. Matendawa amapangitsa kuti minofu isamakule ndiponso imafooka. Zimenezi zinkachititsa kuti a Hartl azisamalira mwanayo ngakhale usiku ndipo usiku wonse iwo ankaonetsetsa kuti mwanayo akupuma bwino komanso ankafunika kuyesetsa kuchotsa zinthu zimene zingatseke paipi ya mpweya pofuna kumuteteza mwanayo kumatenda osiyanasiyana kapena a chibayo. Mwana wina wamwamuna wa mayiwa dzina lake Max analinso ndi matenda a DMD komanso anali ndi matenda a mu ubongo. Mayiwa anasamalira mwachikondi ana awo awiriwa kwa zaka zambiri. Koma chomvetsa chisoni n’chakuti mwana wawo Max anamwalira mu 2008 ali ndi zaka 19.

Mayi Hartl atafunsidwa kuti anene chimene chinkawalimbikitsa kuti azisamalira mwachikondi ana awo, iwo anayankha kuti: “Chifukwa cha zimene ndimaphunzira ku chipembedzo changa. Ndine wa Mboni za Yehova ndipo ndimalemekeza kwambiri moyo. Ndipo ndichita zimene ndingathe kuti mwana wanga azisangalala ndi moyo ngakhale kuti ndi wolumala.”

Nduna yaikulu a Seehofer anayamikira mayi Hartl komanso anthu ena amene analandira mendulo ndipo iwo anati, “Aliyense wa inu wachita zinthu zotamandika m’dziko lino.”

Lankhulani ndi:

Kuchokera m’mayiko ena: J. R. Brown, Office of Public Information, tel. +1 718 560 5000

Germany: Wolfram Slupina, tel. +49 6483 41 3110