Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

JULY 11, 2019
GREECE

Zokhudza Msonkhano wa Mayiko wa 2019 Wakuti “Chikondi Sichitha,” ku Athens, Greece

Zokhudza Msonkhano wa Mayiko wa 2019 Wakuti “Chikondi Sichitha,” ku Athens, Greece
  • Masiku: 5 mpaka 7 July, 2019

  • Malo: Athens Olympic Stadium ku Athens, Greece

  • Zinenero: Chiabaniya, Chingelezi, Chigiriki, Chinenero Chamanja cha ku Greece, Chiromane (cha kum’mwera kwa Greece), Chirasha

  • Chiwerengero cha Osonkhana: 36,873

  • Chiwerengero cha Obatizidwa: 406

  • Chiwerengero cha Alendo Ochokera ku Mayiko Ena: 6,000

  • Nthambi Zoitanidwa: Albania, Armenia, Australasia, Bulgaria, Central America, Central Europe, Fiji, Japan, Kyrgyzstan, North Macedonia, Turkey, United States

  • Zina Zomwe Zinachitika: Munthu wina yemwe amagwira ntchito yopanga dongosolo la maulendo a anthu anati: “Ndakhala ndikugwira ntchitoyi kwa moyo wanga wonse koma sindinaonepo kulikonse padzikoli anthu opanga bwino dongosolo la anthu omwe ali paulendo ngati inuyo. Ndinagoma kwambiri ndi zimene ndinaona mukuchita dzulo. Munapanga dongosolo la mayendedwe la anthu 2,600 m’maola ochepa m’njira yabwino kwambiri kuposa anthu ambiri omwe ndi akatswiri pa ntchitoyi. Koma chinthu chosangalatsa kwambiri ndi kumwetulira kwanu. Zimene ndikunenazi n’zoona chifukwa ndagwira ntchito imeneyi kwa zaka zambiri ndipo ndimadziwa ngati munthu akungomwetulira chifukwa choti akufunika kutero pa ntchito yake kapena ngati akumwetulira zenizeni kuchokera mumtima. Koma nonsenu mumamwetulira kuchokera mumtima.”

 

Ena mwa abale ndi alongo oposa 4,000 ongodzipereka omwe anagwira ntchito yokonza sitediyamu pokonzekera msonkhano.

Achinyamata akulandira alendo omwe anabwera kumsonkhanowu ku Greece

Mmodzi mwa abale ndi alongo atsopano 406 akubatizidwa

Alongo olankhula Chiromane akujambulitsa pamalo a msonkhano. Umenewu unali msonkhano wa mayiko woyamba ku Greece womwe unachitikanso m’chinenero cha Chiromane

Alendo ali limodzi muutumiki ndi abale ndi alongo a ku Greece

Alendo akuona mabwinja akale a ku Greece

Akuchita sewero la m’Baibulo pa nthawi yomwe anthu anakumana pamodzi madzulo. Seweroli linali lofotokoza za utumiki wa Mtumwi Paulo ku Greece.

Abale ndi alongo akusonyeza alendo mmene amavinira gule wotchuka wa Syrtaki

Mlongo akuimba chida choimbira cha ku Greece chotchewa bouzouki

Alendo akuphunzira mawu a chinenero cha Chigiriki

M’bale David Splane wa m’Bungwe Lolamulira akukamba nkhani ya m’Baibulo yomaliza pa tsiku lachiwiri la msonkhano ndipo nkhaniyi inamasuliridwa mu Chigiriki

Abale ndi alongo omwe ali mu utumiki wanthawi zonse wapadera akubayibitsa pa tsiku lomaliza la msonkhanowu